Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/14 tsamba 4
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa March
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 2/14 tsamba 4

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa March

“Tabwera kuti tikambirane nanu mwachidule zokhudza mwambo umene udzachitike pa April 14. Tsiku limeneli ndi lokumbukira imfa ya Yesu. Anthu ena adzafika pa mwambowu chifukwa choti amaona kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Koma ena sadziwa ngati imfa ya Yesu ili yofunika kwambiri kwa anthufe. Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi imfa ya Yesu ingakuthandizeni inuyo komanso ineyo?” Yembekezerani ayankhe. Asonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya March 1, ndipo kambiranani ndime zimene zili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimezo. Agawireni magaziniyo, ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.

Nsanja ya Olonda March 1

“Anthu ambiri amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu sakuthetsa zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto onse amene akuchitika m’dzikoli. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa choti Mulungu alibe nazo ntchito, kapena n’chifukwa choti amaona kuti ndi bwino anthu azivutika? [Yembekezerani ayankhe, ndipo kenako werengani Yohane 3:16.] Ngakhale kuti anthu ambiri amatchula mawu a vesili posonyeza kuti Mulungu amakonda anthu, sadziwa kwenikweni mmene imfa ya Mwana wa Mulungu ingathandizire iwowo. Magaziniyi ikufotokoza mmene imfa ya Yesu idzathandizire kuti zinthu zopanda chilungamo komanso zoipa zonse zithe padzikoli.”

Galamukani! March

“Tabwera kuti tikambirane nanu mwachidule zokhudza zinthu zolakwika zomwe anthu ena amaganiza pa vesi la m’Baibulo ili. [Werengani Genesis 1:1.] Anthu ena amakhulupirira zimene vesili likunena, zoti zinthu zinachita kulengedwa, pamene ena sakhulupirira zimenezi. Inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ena zimawavuta khulupirira zoti zinthu zonsezi zinachita kulengedwa chifukwa choti atsogoleri ena achipembedzo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene Baibulo limanena. Magaziniyi ikufotokoza momveka bwino mmene Mulungu analengera zinthu zonse.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena