Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Pamene mapeto akuyandikira, tiyeni tipitirize kulalikira kwa anthu osiyanasiyana ndipo Yehova adzatidalitsa. Mwachitsanzo, bambo wina wa ku Lizulu anaphunzira choonadi kuchokera kwa wachibale wake. Ngakhale kuti poyamba bamboyu anali Rasi ndipo ankamwa mowa mwauchidakwa komanso kusuta fodya, ataphunzira choonadi anasintha. Iye anabatizidwa mu October 2011 ndipo mkazi wakenso anabatizidwa ku Dedza pa msonkhano wachigawo wa 2013. Panopa m’baleyu ndi mtumiki wothandiza. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosintha anthu. (Aheb. 4:12) Tikuphunziraponso kuti tiziyesetsa kulalikira kwa achibale athu omwe si Mboni.