Ndandanda ya Mlungu wa March 10
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 10
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 14-20 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 40-42 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 41:1-16 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Mmene “Otsala a Akufa” Adzabwererenso Kumoyo Padziko Lapansi—rs tsa. 112 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kuchita Zinthu Motani ndi Munthu Wochotsedwa?—lv tsa. 207-209 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kulambira kwa Pabanja N’kothandiza Kwambiri. Funsani banja lina kuti lifotokoze mmene limachitira kulambira kwa pabanja. Kodi ndi zinthu ziti zimene amachita? Kodi amasankha bwanji nkhani zoti aphunzire? Ndi zinthu ziti za pa webusaiti yathu ya jw.org/ny zimene agwiritsapo ntchito? Nanga zimene amaphunzira zimawathandiza bwanji mu utumiki? Kodi amatani kuti zinthu zina zisawalepheretse kuchita kulambira kwa pabanja? Nanga apindula bwanji chifukwa chochita kulambira kwa pabanja?
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Zimene Tinganene kwa Anthu Amene Sakufuna Kuti Tiwalalikire.” Nkhani yokambirana. Kambiranani mfundo ziwiri kapena zitatu zimene anthu anganene posafuna kuti tiwalalikire ndipo pemphani omvera kuti afotokoze mmene angayankhire ngati munthu atanena zimenezo. Kumbutsani omvera kuti mlungu woyambira April 7, adzakhala ndi mwayi wofotokoza zinthu zosangalatsa zimene akumana nazo pogwiritsa ntchito mfundo za m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero