Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Zimene Tinganene kwa Anthu Amene Sakufuna Kuti Tiwalalikire
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Tayerekezani kuti mwamva kuti m’dera lanu muchitika chivomezi chimene chingaphe anthu ambiri ngati sachoka m’deralo. Ndiye mukuthamangira kwa munthu amene mwayandikana naye nyumba kuti mukamuuze. Koma mutangoyamba kulankhula, iye akukudulani mawu n’kukuuzani kuti alibe nthawi yoti amvetsere zimene mukufuna kumuuzazo. Kodi mungamusiye nthawi yomweyo n’kumapita? Anthu ambiri amakana uthenga wathu chifukwa choti sadziwa kufunika kwa uthengawu. Mwina pa nthawi yomwe tawapeza angakhale kuti ndi otanganidwa ndi zinthu zina. (Mat. 24:37-39) Kapena angakhale kuti anamvapo nkhani zabodza zokhudza Mboni za Yehova. (Mat. 11:18, 19) Akhozanso kumaganiza kuti sitikusiyana ndi anthu a zipembedzo zina zonse amene amachita zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. (2 Pet. 2:1, 2) Ngati munthu amene tikumulalikirayo akukana kukambirana nafe, sitiyenera kungomusiya nthawi yomweyo.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukakumana ndi munthu amene akukana kuti mukambirane naye, mukangosiyana naye, kambiranani ndi amene mwayenda naye njira yabwino imene mukanamuyankhira.