Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tingatani Ngati Tapeza Munthu Waukali?
N’chifukwa Chiyani Kudziwiratu Zochita N’kofunika? Nthawi zambiri anthu amene timawalalikira amakhala aulemu. Komabe Yesu ananeneratu kuti anthu ena azidzadana nafe. (Yoh. 17:14) Choncho sizodabwitsa kuti tikamalalikira, nthawi zina timakumana ndi anthu aukali. Zikatere tiyenera kuchita zinthu zomwe zingasangalatse Yehova, chifukwa tikamalalikira timakhala tikuimira iyeyo. (Aroma 12:17-21; 1 Pet. 3:15) Zimenezi zingathandize kuti zinthu zisafike poipa komanso kuti munthuyo ndi anthu ena aone kuti ndife anthu a Mulungu. Zingathandizenso kuti nthawi ina adzamvetsere.—2 Akor. 6:3.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambira kwa pabanja, yesererani zimene mungachite mukakumana ndi munthu waukali.
Mukachoka panyumba ya munthu yemwe wakuyankhani mwaukali, uzani mnzanu amene mwayenda naye zinthu zina zomwe mumayenera kuchita.