Ndandanda ya Mlungu wa January 12
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 12
Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 7 ndime 1-8 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 21-24 (Mph. 8)
Na. 1: Yoswa 24:14-21 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: N’chiyani Chinathandiza Petulo ndi Yohane Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima?—bt tsa. 31-32 ndime 9-12 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova Ndi Mlengi Wamphamvu Zonse—igw tsa. 2 ndime 4–tsa. 3 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
MUTU WA MWEZI UNO: ‘Tumikirani Ambuye Monga Kapolo Modzichepetsa Kwambiri.’—Mac. 20:19.
Mph. 10: Muzitumikira Ambuye Modzichepetsa Monga Akapolo. Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 20:19. Kenako kambiranani mafunso awa: (1) Kodi mawu akuti “kapolo” amatanthauza chiyani? (2) Kodi tingatumikire Ambuye Yesu Khristu monga akapolo m’njira ziti? (3) Kodi kudzichepetsa kumatanthauza chiyani? (4) Kodi kudzichepetsa kumatithandiza bwanji kuti tizigwirabe ntchito yolalikira?
Mph. 20: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tingatani Ngati Tapeza Munthu Waukali?” Nkhani yokambirana. Mukamaliza kukambirana nkhaniyi, chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Mbali yoyamba isonyeze wofalitsa akuyankha mopanda ulemu munthu waukali. Mbali yachiwiri isonyeze wofalitsayo akuyankha munthu mwaulemu komanso mwaluso. Limbikitsani onse kuti ayesetse kutsatira malangizo omwe ali pansi pa kamutu kakuti, “Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno.”
Nyimbo Na. 76 ndi Pemphero