Muzikambirana Ndi Mwininyumba
1. Tchulani njira yabwino kwambiri kutsatira polalikira mukakhala mu utumiki.
1 Mukakhala mu utumiki, kodi mungatani kuti muzifika pa mtima omvera? Kodi ndi bwino kutsutsa zimene mwininyumba akunena kapena kukambirana naye kuti mupeze mfundo yothandiza? Mtumwi Paulo ankagwiritsa ntchito njira yokambirana ndi ena pamene ankalankhula ndi Ayuda ku Tesalonika ndipo “zotsatira zake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira.” (Mac. 17:2-4) Kodi chimafunika n’chiyani kuti muzitha kukambirana ndi ena?
2. Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Paulo tikamalalikira uthenga wabwino?
2 Ganizirani Mmene Munthuyo Akumvera Ndiponso Moyo Wake: Ngati tikudziwa zimene anthu a m’gawo lathu amakhulupirira ndiponso mmene amaganizira, sitidzavutika kukambirana nawo. Paulo anayamba nkhani imene anakambirana ndi Agiriki ku Areopagi mwa kutchula zinthu zimene anthuwo ankazidziwa ndiponso kuzivomereza. (Mac. 17:22-31) Choncho, mukamakonzekera zokanena, muziganizira zinthu zimene anthu ambiri m’gawo lanu amakhulupirira ndiponso malingaliro olakwika amene ali nawo. (1 Akor. 9:19-22) Ngati mwininyumba wayamba kutsutsa, yesetsani kukambirana naye nkhani imene angaivomereze ndipo kambiranani nkhani imeneyo.
3. Kodi tingakambirane bwanji ndi anthu mogwira mtima pogwiritsa ntchito mafunso mwaluso?
3 Muzigwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso: N’zosatheka kupatsa munthu mapu kuti akafike kumene akufuna ngati ifeyo sitikudziwa malo amene munthuyo ali pa nthawiyo. Mofanana ndi zimenezi, ifenso sitingathe kuthandiza mwininyumba kudziwa zolondola ngati ifeyo sitikudziwa maganizo ake. Yesu asanayambe kukambirana ndi munthu, nthawi zambiri ankafunsa mafunso kuti adziwe zimene munthuyo akuganiza. Mwachitsanzo, munthu wina atafunsa Yesu kuti, “Ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?,” poyamba Yesu anafuna kudziwa zimene munthuyo ankaganiza. (Luka 10:25-28) Pa nthawi ina, Petulo atayankha molakwitsa, Yesu anagwiritsa ntchito mafunso kuti athandize Petulo kuganiza. (Mat. 17:24-26) Choncho, ngati mwininyumba wafunsa funso kapena kufotokoza maganizo olakwika, tingagwiritse ntchito mafunso kuti timuthandize kuganiza pa nkhani ina yake.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mokambirana ndi mwininyumba?
4 Tikathandiza mwininyumba kuganiza ndiye kuti tikutengera chitsanzo cha Mphunzitsi Waluso, Yesu, komanso atumiki ambiri aluso amene anakhalapo m’nthawi ya atumwi. Ndipo tikamachita zimenezi timakhala tikulemekeza mwininyumbayo. (1 Pet. 3:15) Zotsatira zake n’zakuti, mwininyumbayo angatilole kuti tidzabwerenso.