Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/99 tsamba 8
  • Tiyeni ‘Tinene Mfundo Yathu Mwachidule!’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tiyeni ‘Tinene Mfundo Yathu Mwachidule!’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Muzichitira Anthu Zimene Mungafune Kuti Akuchitireni
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Munayamba Mwasonyezapo Munthu pa Ulendo Woyamba Mmene Timachitira Phunziro la Baibulo?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 7/99 tsamba 8

Tiyeni ‘Tinene Mfundo Yathu Mwachidule!’

1 Kodi mwininyumba anayamba wakudulani ulaliki wanu wokonzekera bwinowo ndi mawu akuti: “Kodi mukufuna chiyani? Tanenani mfundo yanu mwachidule!” Kodi tingaphunzireponji pa chokumana nacho chotere?

2 Anthu ambiri lerolino sali oleza mtima. Amafuna kuti atidziŵe ndi chifukwa chake tafikira panyumba pawo. Akadziŵa kuti cholinga chathu ndi kukambirana nawo Baibulo, angakane kumvetsera. Kuŵerenga Baibulo ndi makambitsirano auzimu si zinthu zofunika kwambiri m’miyoyo ya anthu ambiri. Kodi tingawalimbikitse motani eninyumba oterewa kuti ayenera kupatula mphindi zingapo kuti akambirane nafe nkhani za Baibulo?

3 Zimene Zimagwira Ntchito Kwambiri: Njira yake ndiyo kumusonyeza mwininyumba kuti Baibulo limapereka njira zothetsera mavuto amene amam’detsa nkhaŵa, ndipo tichite zimenezi mwachidule mmene tingathere. Ulaliki wogwira mtima kwambiri umakhala ndi funso lachidunji lopangitsa mwininyumba kuganiza, lotsagana ndi lemba loyankha funsolo. Mungasangalale kuyesera malingaliro otsatirawa. Akonzedwa kuti atithandize kufulumira ‘kunena mfundo yathu mwachidule’ tikumadzutsa chidwi cha mwininyumba.

4 Mu gawo limene nthaŵi zambiri anthu amanena kuti sakufuna, dzutsani funso limene limawakhudza paokha:

◼ “Pamene tikuyandikira zaka chikwi zina, kodi muli ndi chiyembekezo kapena nkhaŵa? [Yembekezerani yankho.] Baibulo linaneneratu zinthu zosautsa zimene tikuziona lerolino ndi zotsatirapo zake.” Werengani 2 Timoteo 3:1, 2, 5 ndi Miyambo 2:21, 22.

◼ “M’dziko lino, anthu ali ndi nkhaŵa kwambiri ponena za umoyo. Kodi mukudziŵa kuti Mulungu akulonjeza kuti adzathetseratu matenda onse?” Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.

◼ “Kodi muganiza kuti dera lathu lingapindule bwanji ngati aliyense amene amakhala muno agwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo?” Werengani Mateyu 22:37-39.

5 Popeza ntchito yathu ndi yolalika uthenga wabwino wa Ufumu, paliponse pamene tingathe tiyenera kusonyeza zimene Ufumu udzachita. Munganene kuti:

◼ “Kodi mumadziŵa kuti buku lakale kwambiri padziko lonse, Baibulo, linaneneratu kuti padziko lonse padzakhala boma limodzi?” Werengani Danieli 2:44.

◼ “Kodi muganiza kuti zinthu zikanakhala zotani ngati Yesu Kristu ndiye amalamulira dziko?” Werengani Salmo 72:7, 8.

6 Mu gawo limene anthu ali achipembedzo, mungayese amodzi a mawu oyamba awa:

◼ “Anthu ambiri amasankhana chifukwa chakuti ndi amuna kapena akazi, chifukwa cha chipembedzo, kapena mtundu wa khungu lawo. Kodi muganiza kuti Mulungu amamva bwanji ndi tsankho lotereli?” Werengani Machitidwe 10:34, 35.

◼ “Tikudziŵa kuti Yesu Kristu anachita zozizwitsa zambiri m’tsiku lake. Ngati mukanam’pempha kuchitanso chozizwitsa china, kodi chikanakhala chotani?” Werengani Salmo 72:12-14, 16.

7 Ngati mwininyumba sakufuna kulankhula nanu, mungayambe makambitsirano mwa kunena kuti:

◼ “Anthu ambiri lerolino atopa kumva za mavuto. Akufuna kumva za zothetsera zake. Mosakayikira zili chonchonso kwa inu. Komano n’kuti kumene tingapeze zothetsera zenizeni za mavuto athu?” Yembekezerani yankho. Werengani 2 Timoteo 3:16, 17.

8 Bwanji Osayesa? Nthaŵi zambiri funso losavuta, lachidule ndizo zokha zimafunika kuti tidzutse chidwi cha mwininyumba. Mayi wina amene poyamba ankatsutsa analoŵetsa alongo aŵiri m’nyumba mwake mmodzi wa iwo atamufunsa kuti: “Kodi mungatchule Ufumu umene mumaupempha m’Pemphero la Ambuye?” Mayi uja anachita chidwi ndi funsoli, ndipo anavomera phunziro la Baibulo. Tsopano ndi mtumiki wodzipatulira wa Yehova!

9 Pamene mukulankhula ndi mwininyumba, khalani otsimikiza zimene mukunena. Lankhulani zochokera pansi pa mtima. Anthu savuta kumvetsera pamene aona kuti tili ndi chidwi mwa iwo.—Mac. 2:46, 47.

10 Lerolino ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yovuta. Eninyumba ena amakayikira alendo. Ena moyo wawo ndi wotangwanika ndipo amakhala ndi nthaŵi yochepa. Komabe, tili otsimikiza kuti padakali ambiri oyenerera oti apezeke. (Mat. 10:11) Zoyesayesa zathu zowafunafuna zingakhale zopindulitsa kwambiri ngati tichita ulaliki wachidule ndi ‘kunena mfundo yathu mwachidule!’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena