Ndandanda ya Mlungu wa October 17
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 17
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 14 ndime 10-16 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Miyambo 12-16 (Mph. 10)
Na. 1: Miyambo 15:1-17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Mapemphero Ovomerezeka Ali Ngati Zofukiza Zonunkhira Bwino kwa Yehova?—Sal. 141:2; Chiv. 5:8 (Mph. 5)
Na. 3: N’chiyani Chimene Chikusonyeza Kuti Tikukhala M’masiku Otsiriza?—rs tsa. 261 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 5:11, 12, 14-16, 23, 24. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 10: Lolani Kuti Mwininyumba Aone Yekha. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 145. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akupitanso kwa munthu amene anachita chidwi, koma m’Baibulo lake anachotsamo dzina la Mulungu.
Mph. 10: “Musalephere Kulalikira.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani achikulire komanso ana kuti afotokoze zimene anakumana nazo polalikira ali kusukulu.
Nyimbo Na. 19 ndi Pemphero