“Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse”
1. Kodi tingagwiritse ntchito malangizo a m’Baibulo ati ngati eninyumba akhumudwa chifukwa chowalalikira?
1 Anthu a Yehovafe timakonda mtendere ndiponso uthenga umene timalengeza ndi wa mtendere. (Yes. 52:7) Komabe nthawi zina anthu ena amakhumudwa chifukwa choti tapita kunyumba kwawo kuti tikawalalikire. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tichite zinthu mwamtendere zoterezi zikachitika?—Aroma 12:18.
2. Kodi n’chifukwa chiyani kukhala ozindikira kuli kofunika?
2 Khalani Ozindikira: Ngakhale kuti anthu ena amalusa chifukwa chodana ndi choonadi, ena amatha kulusa pa zifukwa zina osati chifukwa chodana ndi uthenga wathu. Mwina akhoza kulusa chifukwa choti tawapeza pa nthawi yolakwika. Nthawi zina mwininyumba angakhumudwe chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo. Ngakhale atalusa chifukwa chodana ndi uthenga wabwino, tiyenera kukumbukira kuti iye akuchita zimenezo chifukwa choti wasocheretsedwa. (2 Akor. 4:4) Kukhala ozindikira kudzatithandiza kuchita zinthu mwamtendere komanso kudziwa kuti mwininyumbayo sanakhumudwe chifukwa cha ifeyo.—Miy. 19:11.
3. Kodi tingalemekeze bwanji anthu amene timawalalikira?
3 Chitani Zinthu Mwaulemu: Anthu ambiri amene timawalalikira amakhala ndi zikhulupiriro zimene zinazikika molimba mumtima mwawo. (2 Akor. 10:4) Komanso iwo ali ndi ufulu womvetsera kapena kukana uthenga wathu. Chotero tiyenera kupewa kunyoza zimene amakhulupirira kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti ifeyo timadziwa Baibulo kwambiri kuposa iwowo. Ngati atatiuza kuti tichoke panyumba pawo, tiyenera kumvera mwaulemu.
4. Kodi kulankhula mwachisomo kumatanthauza chiyani?
4 Muzilankhula Mwachisomo: Ngakhale eninyumba atatilankhula mwachipongwe, tiyenera kuyankha modekha ndi mwachisomo. (Akol. 4:6; 1 Pet. 2:23) M’malo mokangana nawo, tiyenera kupeza nkhani imene ingathandize kuti tigwirizane. Mwina tingafunse mwininyumba mokoma mtima chifukwa chimene akukanira kuti timulalikire. Koma pofuna kupewa kumukhumudwitsa kwambiri, nthawi zina zimakhala bwino kungotsanzika.—Miy. 9:7; 17:14.
5. Kodi kukhala amtendere mu utumiki kuli ndi ubwino wotani?
5 Ngati titachita zinthu mwamtendere, mwininyumba sangaiwale zimenezi ndipo zingathandize kuti adzamvetsere m’bale wina akadzapita kukamulalikira. (Aroma 12:20, 21) Tizikumbukira kuti ngakhale atakhala wotsutsa kwambiri, tsiku lina akhoza kudzakhala m’bale wathu. (Agal. 1:13, 14) Kaya mwininyumba akane motani, tidzalemekeza Yehova komanso kukometsera chiphunzitso chathu ngati titakhalabe odziletsa komanso titachita zinthu mwamtendere.—2 Akor. 6:3.