Olimba Mtima, Koma Amtendere
1 Anthu ambiri amene timawalalikira, amasonyeza kuti amakhulupirira ndi mtima wonse zinthu zimene n’zotsutsana ndi choonadi cha m’Baibulo. Ngakhale kuti tikufunikira kulalikira molimba mtima, timafunanso ‘kukhala mwa mtendere ndi anthu onse’ ndi kupewa kukhumudwitsa anthu mwadala. (Aroma 12:18; Mac. 4:29) Koma kodi tingalalikire bwanji uthenga wa Ufumu molimba mtima, komanso mwamtendere?
2 Pezani Mfundo Zimene Mungagwirizane: Munthu wamtendere amapewa mikangano. Kutsutsa mwadala zinthu zimene mwininyumba amakhulupirira mwamphamvu, sikungamuchititse kuti amvetsere uthenga wathu. Ngati atatchula zinthu zolakwika, tingachite bwino kuyambitsa nkhani ina imene mwininyumbayonso angagwirizane nayo. Kutsindika mfundo zimene mwininyumba angagwirizane nazo, kungathandize kuchotsa maganizo olakwika alionse amene mwininyumba angakhale nawo pa ife ndipo tingamufike pamtima.
3 Kodi kunyalanyaza zikhulupiriro zolakwika za mwininyumba, ndi kugonja kapena kusukulutsa choonadi? Ayi. Monga atumiki achikhristu, ntchito yathu ndi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, osati kutsutsa maganizo olakwika alionse amene tingamve anthu akunena. (Mat. 24:14) M’malo mokhumudwa tikamva munthu akunena mfundo zolakwika, tiutenge ngati mwayi wathu wodziwira zinthu zimene munthuyo amaganiza.—Miy. 16:23.
4 Apatseni Ulemu: Nthawi zina tingafunikedi kukhala olimba mtima ndi opanda mantha potsutsa ziphunzitso zolakwika. Komabe, monga anthu amtendere, timapewa kunyoza kapena kunyogodola anthu amene amakhulupirira kapena kuphunzitsa zinthu zolakwika. Mtima wodzimva umathawitsa anthu, koma kudzichepetsa ndi kukoma mtima kumatsegula mitima ya anthu okonda choonadi. Kulemekeza omvera athu ndi zikhulupiriro zawo, kumakhala kuwasungira ulemu wawo, ndipo zimakhala zosavuta kuti amvetsere uthenga wathu.
5 Mtumwi Paulo ankaganizira kaye zikhulupiriro za anthu amene ankawalalikira ndipo ankafufuza njira yowalalikirira mowafika pamtima. (Mac. 17:22-31) Anasankha kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana,” kuti ‘mulimonse mmene zingakhalire apulumutsepo ena.’ (1 Akor. 9:22) Nafenso tingachite chimodzimodzi mwa kulalikira uthenga wabwino mwamtendere ndi molimba mtima.