Ndandanda ya Mlungu wa March 17
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 17
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 9 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 43-46 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 44:18-34 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ndi Anthu Enanso Ati Amene Adzaukitsidwa Kuti Akhale Ndi Moyo Padziko Lapansi?—rs tsa. 113 ndime 1-5 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupitiriza Kudalira Yehova?—bh tsa. 164-165 ndime 1-4 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Muzichita Zinthu Mosamala Mukamalalikira. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 197, ndime 1 mpaka 199, ndime 4. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuyankha mwachisawawa munthu amene akutsutsa uthenga wa m’Baibulo. Kenako chitaninso chitsanzo china chosonyeza wofalitsayo akuyankhanso munthuyo mosamala kwambiri.
Mph. 15: “Kodi Mudzachita Zinthu Zosonyeza Kuyamikira Yehova pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene azidzawerengera Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wakonza kudzachita pa nyengoyi.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero