Nyimbo 97
Pitani Patsogolo, Inu Atumiki a Ufumu!
1. Pitani patsogolo ndithu
Polalikira konse.
Muthandize anthu ofatsa
Cho’nadi achikonde.
Ndi mwayidi kutumikira,
Tikonda kulalikira.
Chitirani umboni M’lungu
Ndi dzina lake loyera.
(KOLASI)
Pitirizani kulalikira
padziko lonse.
Pitirizani kukhala
okhulupirikabe.
2. Atumiki enieninu
Pitani patsogolo.
Timatsatira Mbuye wathu.
Tidzalandira mphoto.
Ndi kofunika kuti anthu
Amve uthenga wa M’lungu.
Yehova atipatsa mphamvu
Ndipo sitiopa kanthu!
(KOLASI)
Pitirizani kulalikira
padziko lonse.
Pitirizani kukhala
okhulupirikabe.
3. Tipite patsogolo tonse,
Amuna ndi akazi.
Otsalira ndi nkhosa zina
Tiziyenda m’cho’nadi.
Wathu si utumiki wamba.
Kwa ife n’ngopatulika.
Tiyeni tisonyeze M’lungu
Kuti ndife oyenera.
(KOLASI)
Pitirizani kulalikira
padziko lonse.
Pitirizani kukhala
okhulupirikabe.
(Onaninso Sal. 23:4; Mac. 4:29, 31; 1 Pet. 2:21.)