Nyimbo 50
Mulungu Anatipatsa Chitsanzo Pankhani Yosonyeza Chikondi
Losindikizidwa
1. M’lungu mwanzeru watipatsa tonse
Chitsanzo,
Tonsefe,
Inde pankhani yokhudza chikondi
Kuti ife,
Tisagwetu.
Yendani m’njira ya M’lungu yabwino,
Yolimbikitsa kuchita zabwino,
Ndi yamtendere, yogwirizanitsa.
Yachikondi.
Yachikondidi.
2. Tikamayenda munjira ya M’lungu
Tikonde
Abale,
Zitichititse kuthandizanadi
Nthawi zonse,
Nthawi zonse.
Zitichititse kukhululukira,
Tidzafanana ndi Mulungu wathu
Poonetsatu chikondi kwa ena,
Makamaka,
Abale athu.
3. Kukonda M’lungu kutilimbikitsa,
Indedi,
Ndithudi.
Mosangalala, timadzipereka
Pom’tamanda,
Pom’tamanda.
Dzina lakelo tililengezetu
Kuti enanso adziwe cho’nadi.
Tipitirize kum’tumikirabe,
Chimenecho,
Ndicho chikondi.
(Onaninso Aroma 12:10; Aef. 4:3; 2 Pet. 1:7.)