Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Pogawira Kapepala Koitanira Anthu ku Chikumbutso
“Tikugawa timapepala tokuitanirani ku mwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike pa April 14. Pa tsikuli, anthu ambirimbiri padziko lonse adzasonkhana kuti akumbukire imfa ya Yesu Khristu komanso kuti amvetsere kwaulere nkhani ya m’Baibulo yofotokoza mmene imfa ya Yesu imatithandizira. Pakapepalaka talembapo malo ndi nthawi yomwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino.”
Nsanja ya Olonda April 1
“Takupezani kuti tikambirane mwachidule zokhudza pemphero. Pafupifupi munthu aliyense, kaya ndi wachipembedzo chanji, anapempherapo. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amayankha mapemphero, kapena pemphero limangotithandiza kuti mtima wathu ukhale m’malo tikakhala ndi mavuto? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero. [Werengani 1 Yohane 5:14.] Magaziniyi ikufotokoza mmene pemphero limathandizira.”
Galamukani! April
“Tabwera kuti tikambirane nanu za vuto limene lili ponseponse masiku ano. Anthu ena amasowa mtengo wogwira chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo moti mpaka amaganiza zongodzipha. Koma kodi mukuganiza kuti anthu oterewa amakhaladi kuti akufuna kufa, kapena kwenikweni amakhala kuti akungofuna kuthana ndi mavuto awowo? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani lemba la m’Baibulo ili, lomwe lathandiza anthu ambiri kuti ayambe kuona zinthu moyenera. [Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Magaziniyi ikufotokoza zifukwa zitatu zimene zingathandize munthu kuona kuti si bwino kudzipha ngakhale kuti akukumana ndi mavuto.”