Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/13 tsamba 4
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 2/13 tsamba 4

Zitsanzo za Ulaliki

Zomwe Tinganene Poitanira Anthu ku Chikumbutso

“Tabwera n’cholinga choti tikupatseni kapepala aka, koitanira inuyo pamodzi ndi banja lanu ku mwambo wofunika kwambiri, womwe umachitika chaka chilichonse padziko lonse. Mwambo wake ndi wokumbukira imfa ya Yesu. Chaka chino mwambo umenewu uchitika pa March 26. Pa mwambowu padzakambidwa nkhani yochokera m’Baibulo yomwe idzafotokoze mmene imfa ya Yesu imatithandizira. Simudzafunikira kulipira ndalama iliyonse kuti mumvere nkhaniyi. Kapepalaka kakusonyeza nthawi ndi malo amene kukachitikire mwambowu m’dera lino.”

Nsanja ya Olonda March 1

“Anthu ena akhala akufunsa funso ili, ‘Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu anaukitsidwa?’ Kodi inuyo munayamba mwaganizirapo funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chake yankho la funso limeneli lili lofunika kwambiri. [Werengani 1 Akorinto 15:20-22.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zimatithandiza kudziwa kuti nkhani yoti Yesu anaukitsidwa siyongopeka koma ndi yeniyeni.”

Galamukani! March

“Kodi mungavomereze mfundo yakuti masiku ano kusamalira banja si ntchito yamasewera? [Yembekezani ayankhe.] Makolo ambiri aona kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza. Mwachitsanzo, vesi ili lathandiza abambo ambiri kuti azipeza nthawi yoti aziyamikira ana awo komanso kuwalimbikitsa. [Werengani Akolose 3:21.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zisanu zofunika kwambiri zimene zingathandize abambo kusamalira bwino ana awo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena