Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu March ndi April: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! May ndi June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena timapepala totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani? kapena kakuti Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
◼ Chikumbutso chidzachitika Lolemba pa April 14, 2014. Ngati mpingo wanu umachita misonkhano Lolemba, mungakonze zoti misonkhanoyi idzachitike tsiku lina mlungu womwewo. Koma ngati n’zosatheka kuchita misonkhanoyi m’kati mwa mlunguwo, wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu angasankhe nkhani za mu Msonkhano wa Utumiki zimene akuona kuti n’zothandiza kwambiri ku mpingo wanu, kuti zikambidwe mlungu wina m’mwezi womwewo.
◼ Kuyambira mwezi wa March 2014, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Posachedwapa Tipulumutsidwa M’dziko la Mavutoli.”