Ndandanda ya Mlungu wa April 7
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 7
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 10 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 7–10 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 9:20-35 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Mmene Kubweranso kwa Yesu Kudzakhalire Ndiponso Mmene Diso Lililonse Lidzamuonere—rs tsa. 163 ndime 3–tsa. 164 ndime 4 (Mph. 5)
Na. 3: Muzikhala Wokhulupirika Ndiponso Wokonzeka Kuthandiza Abale Anu—lv tsa. 33-34 ndime 16-18 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a April. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto. Pomaliza, limbikitsani ofalitsa kuti awerenge ndi kudziwa bwino nkhani za m’magaziniwa komanso kuti adzagawire nawo.
Mph. 10: Musaiwale Kuchereza Alendo. (Aheb. 13:1, 2) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Kumbutsani mpingo zomwe zakonzedwa kudzachitika pa nyengo ya Chikumbutso. Fotokozani njira zimene tingadzasonyezere kuchereza alendo komanso ofalitsa ofooka amene adzafike pa mwambowu. Chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Chitsanzo choyamba chisonyeze wofalitsa akulandira munthu amene analandira kapepala komuitanira ku Chikumbutso. Chitsanzo chachiwiri chisonyeze wofalitsayo, pambuyo pa mwambowu akukonza zoti adzakumanenso ndi munthu uja.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Zimene Tinganene kwa Anthu Amene Sakufuna Kuti Tiwalalikire.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
Nyimbo Na. 20 ndi Pemphero