Kubweranso kwa Kristu
Tanthauzo: Asanachoke padziko lapansi, Yesu Kristu analonjeza kubweranso. Zochitika zochititsa nthumanzi zogwirizanitsidwa ndi Ufumu wa Mulungu nzogwirizanitsidwa ndi lonjezo limenelo. Kuyenera kudziŵika kuti pali kusiyana pakati pa kudza ndi kukhalapo. Chotero, pamene kuli kwakuti kudza kwa munthu (kogwirizanitsidwa ndi kufika kapena kubwerera kwake) kumawonekera panthaŵi yotchulidwa, kukhalapo kwake kungakhaleko kwanyengo yokwanira zaka zambiri pambuyo pake. M’Baibulo liwu Lachigiriki erʹkho·mai (kutanthauza “kudza”) likugwiritsiridwanso ntchito kunena kupereka chisamaliro kwa Yesu kuntchito yofunika panthaŵi yeniyeni mkati mwa kukhalapo kwake, ndiko kuti, kuntchito yake monga wolipsira wa Yehova pankhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.
Kodi zochitika zogwirizanitsidwa ndi kukhalapo kwa Kristu zimachitika m’nthaŵi yaifupi kwambiri kapena mkati mwa nyengo yazaka zambiri?
Mat. 24:37-39, NW: “Monga momwe analiri masiku a Nowa, chotero kudzakhala kukhalapo [“kudza,” RS, TEV; “kukhalapo,” Yg, Ro, ED; Chigiriki, pa·rou·siʹa] kwa Mwana wamunthu. Pakuti monga mmene analiri m’masikuwo chigumula chisanafike, kudya ndi kumwa, amuna kukwatira ndi akazi kukwatiŵa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa; ndipo iwo sanazindikire konse kufikira chigumula chinadza nichinasesa iwo onse, ndimo mmene kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalira.” (Zochitika za “masiku a Nowa” zolongosoledwa panopa zinachitika kwa nyengo ya zaka zambiri. Yesu anayerekezera kukhalapo kwake ndi zimene zinachitika kumbuyoko panthaŵiyo.)
Pa Mateyo 24:37 liwu Lachigiriki lakuti pa·rou·siʹa lagwiritsiridwa ntchito. Kwenikweni limatanthauza “kukhala pandunji.” Greek-English Lexicon ya Liddell ndi Scott (Oxford, 1968) imapereka “kukhalapo, kwa anthu,” monga tanthauzo lake loyamba la pa·rou·siʹa. Lingaliro la liwuli lasonyezedwa momvekera bwino pa Afilipi 2:12, kumene Paulo akusiyanitsa kukhalapo kwake (pa·rou·siʹa) ndi kusakhalapo kwake (a·pou·siʹa). Kumbali ina, m’Mateyu 24:30, amene amasimba za “Mwana wamunthu alinkudza pamitambo yakumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” monga wolipsira wa Yehova pankhondo ya Armagedo, liwu Lachigiriki er·khoʹme·non likugwiritsiridwa ntchito. Omasulira ena amagwiritsira ntchito ‘kudza’ kaamba ka mawu aŵiriwo Achigiriki, koma awo amene ali osamala kwambiri amasonyeza kusiyana pakati pa aŵiriwo.
Kodi kubwerera kwa Kristu kudzakhala mu mpangidwe wowoneka kumaso aumunthu?
Yoh. 14:19: “Katsala kanthaŵi, ndipo dziko lapansi silindiwonanso ine; koma inu [atumwi okhulupirika a Yesu] mundiwona; popeza ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.” (Yesu anali atalonjeza atumwi ake kuti akabweranso ndi kuwatengera kumwamba kukakhala naye. Iwo akanakhoza kumuwona chifukwa chakuti akakhala zolengedwa zauzimu monga momwe iye aliri. Koma dziko silikanamuwonanso. Yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:16.)
Mac. 13:34: “[Mulungu] anamuukitsa iye [Yesu] kwa akufa, wosabwereranso ku chivundi.” (Mwachibadwidwe matupi aumunthu ngokhoza kuvunda. Ndicho chifukwa chake 1 Akorinto 15:42, 44 amagwiritsira ntchito liwu lakuti “chivundi” m’kulankhula koyenderana ndi “thupi lachibadwidwe.” Yesu sadzakhalanso ndi thupi lotero.)
Yoh. 6:51: “Mkate wa moyo wotsika kumwamba ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wadziko lapansi.” (Pokhala ataupereka, Yesu samautenganso. Iye mwakutero sakulanda anthu phindu la nsembe ya moyo wake waumunthu wangwiro.)
Wonaninso tsamba 213-215, pamutu wakuti “Kutengedwa m’Thupi.”
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la kudza kwa Yesu “momwemo” monga momwe anakwerera kumwamba?
Mac. 1:9-11: “Ali chipenyerere iwo [atumwi a Yesu], ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumchotsa kumaso kwawo. Ndipo pa kukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka iye, tawonani, amuna aŵiri ovala zoyera anaimirira pambali pawo; amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba.” (Tawonani kuti apa pamati “momwemo,” osati thupi limodzimodzilo. Kodi iye anakwera mu ‘mkhalidwe’ wotani? Monga momwe vesi 9 limasonyezera, iye anazimiririka pamaso pawo, kuchoka kwake kukumawonedwa kokha ndi ophunzira ake. Dziko lonselo silinazindikire chimene chinachitika. Kukakhalanso kofanana ndi kubweranso kwa Kristu.)
Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa ‘kudza pamitambo’ ndipo ‘diso lirilonse likumamuwona’?
Chiv. 1:7: “Tawonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lirilonse lidzampenya iye, iwo onse amene anampyoza; ndipo mafuko onse apadziko adzamlira iye.” (Ndiponso Mateyu 24:30; Marko 13:26; Luka 21:27)
Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi “mitambo”? Kusawoneka. Pamene ndenge iri m’mtambo wakuda bii kapena kutseri kwa mitambo, kaŵirikaŵiri anthu okhala padziko sangathe kuiwona, ngakhale kuti iwo angamve kulirima kwa mainjini. Yehova anauza Mose kuti: “Ndikudza kwa iwe m’mtambo wakuda bii.” Mose sanawone Mulungu, Koma mtambo umenewo unasonyeza kukhalapo kosawoneka kwa Yehova. (Eks. 19:9; wonaninso Levitiko 16:2; Numeri 11:25.) Ngati Kristu anali kuzadza m’miyamba mowonekera, kuli kwachiwonekere kuti si “diso lirilonse” limene likadamuwona. Mwachitsanzo, ngati anawonekera cha ku Australia, iye sakanakhala wowoneka ku Ulaya, Afirika, ndi ku maiko a Amereka, kodi sichoncho?
Kodi ‘diso lirilonse likamuwona’ mlingaliro lotani? Iwo adzazindikira kuchokera ku zochitika padziko lapansi kuti wakhalako mosawoneka. Ndiponso posonya kumalo amene saali akuthupi, Yohane 9:41 akusimba kuti: “Yesu anati kwa iwo [Afarisi], mukadakhala wosawona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, tipenya: tchimo lanu likhala.” (Yerekezerani ndi Aroma 1:20.) Pambuyo pa kubweranso kwa Kristu, anthu ena amasonyeza chikhulupiriro; amazindikira chizindikiro cha kukhalapo kwake. Ena amakana umboniwo, koma pamene Kristu ayamba kuchitapo kanthu monga wolipsira wa Mulungu pa oipa, ngakhale iwowo adzazindikira mwa chisonyezero cha mphamvu yake kuti chiwonongeko sichiri chochokera kwa anthu koma chochokera kumwamba. Iwo adzadziŵa chimene chikuchitika chifukwa chakuti anachenjezedwa pasadakhale. Chifukwa cha zimene zikuwachitikira, iwo “adzamlira iye.”
Kodi ndani amene “anampyoza”? Kwenikweni, anali asirikali a Roma amene anachita izi panthaŵi ya kuphedwa kwa Yesu. Koma iwo akhala akufa kwanthaŵi yaitali. Chotero izi ziyenera kukhala zikusonya anthu amene amamchitira chipongwe mofananamo, kapena ‘kupyoza,’ otsatira owona a Kristu mkati mwa “masiku otsiriza.”—Mat. 25:40, 45.
Kodi kunganenedwedi kuti munthu ‘wadza’ kapena kuti ‘alipo’ ngati ali wosawoneka?
Mtumwi Paulo analankhula za ‘kusakhalapo m’thupi koma kukhalapo mu mzimu’ ndi mpingo wa Akorinto.—1 Akor. 5:3.
Yehova analankhula za ‘kutsika’ kwake kukasokoneza chinenero cha omanga nsanja ya Babele. (Gen. 11:7) Iye ananenso kuti ‘akatsika’ kulanditsa Aisrayeli ku ukapolo wa Igupto. Ndipo Mulungu anatsimikizira Mose kuti, ‘ine mwinine ndidzamka’ kukatsogoza Israyeli m’Dziko Lolonjezedwa. (Eks. 3:8; 33:14) Koma palibe munthu amene anayamba wawonapo Mulungu.—Eks. 33:20; Yoh. 1:18.
Kodi nchiyani chimene chiri zina za zochitika zimene Baibulo limagwirizanitsa ndi kukhalapo kwa Kristu?
Dan. 7:13, 14: “Anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wamunthu [Yesu Kristu] nafika kwa Nkhalamba yakale lomwe [Yehova Mulungu] ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe, amtumikire.”
1 Ates. 4:15, 16: “Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka.” (Motero, awo amene adzalamulira ndi Kristu adzaukitsidwa kuti akhale naye kumwamba—choyamba awo amene anali atafa m’zaka zochuluka kalero ndiyeno amene akafa pambuyo pa kubweranso kwa Ambuye.)
Mat. 25:31-33: “Pamene Mwana wa munthu adzadza muulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pachimpando chake cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu amitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”
2 Ates. 1:7-9: “Kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo amphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wamphamvu yake.”
Luka 23:42, 43: “Ndipo ananena [wochita zoipa womvera chifundo wokhomeredwa pambali pa Yesu], Yesu, ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu. Ndipo iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe lerolino, udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Pansi pa ulamuliro wa Yesu, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso; akufa amene ali m’chikumbukiro cha Mulungu adzaukitsidwa limodzi ndi mwaŵi wa kusangalala ndi moyo wangwiro padziko lapansi kosatha.)
Wonaninso tsamba 261-266, pamutu wakuti “Masiku Otsiriza.”