Kukhalapo kwa Mesiya ndi Ulamuliro Wake
“Yesu amene walandiridwa kumka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba.”—MACHITIDWE 1:11.
1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene angelo aŵiri anatonthozera atumwi a Yesu pamene iye anakwera kumwamba? (b) Kodi ndimafunso otani amene akudzutsidwa ndi chiyembekezo cha kubweranso kwa Kristu?
AMUNA khumi ndi mmodzi anali mmunsi cha kummaŵa kwa Phiri la Azitona, akuyang’ana dwii kumwamba. Nthaŵi yochepa chabe yapitayo, Yesu Kristu anali atanyamuka pakati pawo, mawonekedwe ake anali kuzimiririka kufikira ataphimbidwa ndi thambo. M’zaka zawo limodzi naye, amuna ameneŵa anali atawona Yesu akupereka umboni wochuluka wakuti iye anali Mesiya; iwo anawona ngakhale mavuto a imfa yake ndi chikondwerero cha chiukiriro chake. Tsopano anali atapita.
2 Angelo aŵiri anawonekera mwadzidzidzi nalankhula mawu otonthoza awa: “Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita kumwamba.” (Machitidwe 1:11) Kunali kolimbikitsa chotani nanga—kukwera kumwamba kwa Yesu sikunatanthauze kuti iye anali atathana ndi dziko lapansi ndi anthu! Mmalo mwake, Yesu akabweranso. Mosakaikira mawu ameneŵa anadzaza atumwiwo ndi chiyembekezo. Mamiliyoni ambiri a anthu lerolino amawona lonjezo la Kristu la kubweranso kukhala lofunika kwambiri. Ena amalankhula za iro monga “Kudza Kwachiŵiri” kapena “Kubweranso.” Komabe, ochulukitsitsa, akuwonekera kukhala osokonezeka maganizo ndi zimene kwenikweni kubweranso kwa Kristu kumatanthauza. Kodi Kristu akubweranso m’njira yotani? Liti? Ndipo kodi ndimotani mmene zimenezi zimayambukirira miyoyo yathu lerolino?
Mmene Kristu Akubwerera
3. Kodi anthu ambiri amakhulupiriranji ponena za kubweranso kwa Kristu?
3 Malinga ndi bukhu lakuti An Evangelical Christology, “kudza kwachiŵiri kapena kubweranso kwa Kristu (parousia) kukukhazikitsa ufumu wa Mulungu, potsirizira, poyera, ndi kuumuyaya wonse.” Chiri chikhulupiriro chovomerezedwa mofala chakuti kubweranso kwa Kristu kudzakhala kowoneka poyera, kowonedwa ndi maso ndi aliyense wokhala papulanetili. Kuti achirikize lingaliro limeneli, ambiri amasonya ku Chivumbulutso 1:7, pamene pamati: “Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lirilonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza.” Koma kodi vesi limeneli liyenera kulingaliridwa monga momwe liliri?
4, 5. (a) Kodi timadziŵa motani kuti Chivumbulutso 1:7 sichiyenera kutanthauziridwa monga momwe chiriri? (b) Kodi ndimotani mmene mawu a Yesu iyemwiniyo amatsimikizirira chidziŵitso chimenechi?
4 Kumbukirani, bukhu la Chivumbulutso linaperekedwa ‘m’zizindikiro.’ (Chivumbulutso 1:1) Pamenepa, ndime imeneyi, iyenera kukhala yophiphiritsira; ndiiko komwe, kodi ndimotani mmene “iwonso amene anampyoza” akawonera Kristu akubweranso? Iwo akhala akufa pafupifupi zaka mazana 20! Ndiponso, angelo ananena kuti Kristu akabwerera “momwemo” monga mmene anapitira. Eya, kodi iye anapita motani? Kodi panali mamiliyoni ambiri openyerera? Ayi, okhulupirika ochepekera chabe ndiwo amene anawona chochitikacho. Ndipo pamene angelo analankhula nawo, kodi atumwiwo anali kuwona ndi maso ulendo wonse wa Kristu womka kumwamba? Ayi, thambo linaphimba ndi kubisa Yesu. Nthaŵi ina pambuyo pake, iye ayenera kukhala atalowa kumwamba kwauzimu monga cholengedwa chauzimu, chosakhoza kuwonedwa ndi maso aumunthu. (1 Akorinto 15:50) Chotero, kwenikweni, atumwiwo anangowona chiyambi chokha cha ulendo wa Yesu; iwo sakanatha kuwona mapeto ake, kubwerera kwake kumwamba kokhala Atate wake, Yehova. Akanatha kuzindikira kokha zimenezi ndi maso awo achikhulupiriro.—Yohane 20:17.
5 Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu akubwerera m’njira yofananayo. Yesu iyemwiniyo ananena mwamsanga asanafe kuti: “Katsala kanthaŵi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine.” (Yohane 14:19) Iye ananenanso kuti “Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe.” (Luka 17:20) Pamenepa, kodi nanga ndimlingaliro lotani, kuti ‘diso lirilonse lidzamuwona’? Kuti tiyankhe, choyamba tifunikira kumvetsetsa bwino za liwu limene Yesu ndi otsatira ake anagwiritsira ntchito ponena za kubweranso kwake.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji mawu onga “kubweranso,” “kudza,” “kufika,” ndi “kubwera” sali matembenuzidwe okwanira a liwu Lachigiriki lakuti pa·rou·siʹa? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti pa·rou·siʹa, kapena “kukhalapo,” kuli kwanthaŵi yaitali kwambiri koposa chochitika chakanthaŵi chirichonse?
6 Chenicheni nchakuti, Kristu akuchita zambiri koposa “kubweranso” kokha. Liwu limenelo, mofanana ndi “kudza,” “kufika,” kapena “kubwera,” limasonya ku chochitika chimodzi m’mphindi yochepa yanthaŵi. Koma liwu Lachigiriki limene Yesu ndi otsatira ake anagwiritsira ntchito limatanthauza zambiri kuposa apa. Liwulo nlakuti pa·rou·siʹa, kwenikweni likumatanthauza “kukhala pambali” kapena “kukhalapo.” Akatswiri ambiri akuvomereza kuti liwu limeneli limagwirizana osati kokha ndi kufika komanso ndi kukhalapo kotsatira—monga pakuchezetsa Boma kwa munthu wachifumu. Kukhalapo kumeneku sikuli chochitika chakanthaŵi; iri nyengo yapadera, nyengo yolinganizidwa yanthaŵi. Pa Mateyu 24:37-39, (NW), Yesu ananena kuti “kukhalapo [pa·rou·siʹa] kwa Mwana wa munthu” kukakhala monga “masiku a Nowa” amene anathera m’Chigumula. Nowa anali kumanga ngalaŵa ndi kuchenjeza oipa kwazaka makumi ambiri Chigumula chisanafike ndi kusesa dongosolo ladziko loipa limenelo. Pamenepa, mofananamo, kukhalapo kosawoneka kwa Kristu kukutha nyengo ya zaka makumi ambiri nakonso kusanathere m’chisautso chachikulu.
7. (a) Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti pa·rou·siʹa siyowoneka ndi maso aumunthu? (b) Kodi ndimotani ndipo ndiliti pamene malemba amene amafotokoza kubweranso kwa Kristu kukhala kowoneka ndi “diso lirilonse” adzakwaniritsidwa?
7 Mosakaikira, pa·rou·siʹa kwenikweni siyowoneka ndi maso aumunthu. Ngati inali yotero, kodi nchifukwa ninji Yesu akanathera nthaŵi yaitali chotero, monga momwe tidzawonera, akumapereka chizindikiro kwa ophunzira ake chowathandiza kuzindikira kukhalapo kumeneku?a Komabe, pamene Yesu adza kudzawononga dongosolo la dziko la Satana, kukhalapo kwake kwenikweni kudzazindikirika kwa onse mosakanika. Ndipanthaŵiyo kuti “diso lirilonse lidzamuwona.” Ngakhale otsutsa a Yesu adzakhoza kuzindikira, mothedwa nzeru, kuti kulamulira kwa Kristu kuli kwenikweni.—Wonani Mateyu 24:30; 2 Atesalonika 2:8; Chivumbulutso 1:5, 6.
Kodi Kumayamba Liti?
8. Kodi ndichochitika chiti chimene chimasonyeza chiyambi cha kukhalapo kwa Kristu, ndipo kodi nkuti kumene zimenezi zinachitikira?
8 Kukhalapo kwa Mesiya kumayamba ndi chochitika chimene chikukwaniritsa mutu wankhani wobwerezedwabwerezedwa wa maulosi Aumesiya. Iye akuvekedwa korona monga Mfumu kumwamba. (2 Samueli 7:12-16; Yesaya 9:6, 7; Ezekieli 21:26, 27) Yesu iyemwiniyo anasonyeza kuti kukhalapo kwake kukagwirizanitsidwa ndi kukhala kwake mfumu. M’mafanizo angapo, anadziyerekezera iyemwini ndi mbuye amene akusiya banja lake ndi akapolo, akuyenda ulendo wanthaŵi yaitali kumka ku “dziko lakutali” kumene akulandira “mphamvu yaufumu.” Iye anapereka fanizo loterolo monga mbali ya yankho lake kufunso la atumwi ake lonena za kuti ndiliti pamene pa·rou·siʹa yake ikayamba; lina analipereka chifukwa chakuti ‘iwo anali kulingalira kuti ufumu wa Mulungu unali kudzayamba nthaŵi yomweyo.’ (Luka 19:11, 12, 15; Mateyu 24:3; 25:14, 19) Chotero, panthaŵi ya kukhala kwake padziko lapansi monga munthu, kuvekedwa kwake korona monga mfumu kunali chikhalirebe mtsogolo, kodzachitika ‘kudziko lakutali’ la kumwamba. Kodi ndiliti pamene kukachitika?
9, 10. Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Kristu tsopano akulamulira kumwamba, ndipo kodi ndiliti pamene iye anayamba ulamuliro wake?
9 Pamene ophunzira a Yesu anamfunsa kuti: “Kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo iri lazinthu?” Yesu anayankha mwa kuwapatsa chidziŵitso chatsatanetsatane cha nthaŵi yamtsogolo imeneyo. (Mateyu, chaputala 24; Marko, chaputala 13; Luka, chaputala 21; wonaninso 2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso, chaputala 6.) Chizindikiro chimenechi chikufotokoza zochitika zatsatanetsatane wa nyengo yamavuto. Ndinthaŵi yosonyezedwa mwa nkhondo za m’mitundu yonse, kuwanda kwa chiwawa, kunyonyosoka kwa moyo wabanja, miliri yamatenda, njala, ndi zivomezi—osati monga mavuto a m’malowo koma monga zipwirikiti zokantha dziko lonse. Kodi zimenezi zikumvekera kukhala zofala? Tsiku lirilonse lopita limatsimikizira kuti zaka za zana la 20 zikuyenererana ndendende ndi mafotokozedwe a Yesu.
10 Olemba mbiri akuvomereza kuti 1914 inali posinthira m’mbiri ya anthu, chaka chosinthira chimene ambiri a mavuto ameneŵa anayamba kukhala osalamulirika, akumachuluka pamlingo wa padziko lonse lapansi. Inde, zochitika zadziko zenizenizo mokwaniritsa ulosi Wabaibulo zonsezo zikusonya ku 1914 kukhala chaka chimene Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu m’mwamba. Ndiponso, ulosi wa Danieli chaputala 4 ukupereka umboni wa kaŵerengedwe kazaka umene umatitsogolera kuchaka chimodzimodzicho—1914—kukhala nthaŵi pamene Mfumu yoikidwa ya Yehova ikayamba ulamuliro wake.b
Kodi Nkukhaliranji Nthaŵi ya Mavuto?
11, 12. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kwa ena kukhulupirira kuti Kristu akulamulira kumwamba tsopano lino? (b) Kodi ndimotani mmene tingafotokozere mwafanizo zimene zinachitika pambuyo poti Yesu wavekedwa korona kukhala Mfumu?
11 Komabe, ena akudabwa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji dziko liri lodzala ndi mavuto chotero ngati Mesiya akulamulira kumwamba? Kodi ulamuliro wake ngwosagwira mtima?’ Kufotokozedwa mwafanizo kungathandize. Dziko likulamuliridwa ndi pulezidenti woipa. Iye anayambitsa dongosolo loipa lokhala ndi zisonkhezero zofikira kungodya iriyonse ya dzikolo. Koma masankho akuchitidwa; munthu wabwino akupambana. Kenaka chiyani? Monga momwe zimakhalira m’maiko ena ademokrase, nyengo ya kusintha ya miyezi ingapo imakhalapo pulezidenti watsopano asanalongedwe. Kodi anthu aŵiriŵa adzachita motani mkati mwa nyengoyi? Kodi mwamuna wabwinoyo adzaukira panthaŵi yomweyo ndi kuthetsa zoipa zonse zimene mnzake wolowedwa maloyo anapanga m’dziko lonselo? Kodi iye, mmalo mwake, sakasumika maganizo ake pamalikulu choyamba, akumakhazikitsa nduna zake zaboma zatsopano ndi kuthetsa migwirizano ndi akuluakulu ndi mandoda autambwali a pulezidenti woyambayo? Motero, pamene alamulira kotheratu, angathe kuyendetsa zinthu kuchokera pamalikulu a ulamuliro oyera, wolama. Ponena za pulezidenti woipayo, kodi iye sakagwiritsira ntchito nyengo yochepa yotsala kudzipezera m’dzikolo mapindu onse opezedwa mwauphyuta amene iye angathe asanataikiridwe ndi ulamuliro wonse?
12 Kwenikweni, nzofanana ndi pa·rou·siʹa wa Kristu. Chivumbulutso 12:7-12 chimasonyeza kuti pamene Kristu anapangidwa kukhala Mfumu kumwamba, choyamba anathamangitsa Satana ndi ziŵanda kumwamba, mwa kutero akumayeretsa malo a Boma Lake. Pokhala atavutika ndi kugonjetsedwa koyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali kumeneku, kodi ndimotani mmene Satana akadzisungira mkati mwa “kanthaŵi” Kristu asanagwiritsire ntchito ulamuliro wake wonse pano padziko lapansi? Mofanana ndi pulezidenti woipa uja, iye akuyesayesa kupeza zonse zimene angathe m’dongosolo lakale lino. Iye sakufuna ndalama; iye akufuna miyoyo ya anthu. Akufuna kuchotsa anthu ambiri monga momwe kungathekere kwa Yehova ndi Mfumu Yake yolamulira.
13. Kodi ndimotani mmene Malemba amasonyezera kuti chiyambi cha ulamuliro wa Kristu chikakhala nthaŵi yovuta pano padziko lapansi?
13 Pamenepa, mposadabwitsa, kuti kuyambika kwa ulamuliro wa Mesiya kumatanthauza nthaŵi ya “tsoka mtunda.” (Chivumbulutso 12:12) Mofananamo, Salmo 110:1, 2, 6 likusonyeza kuti Mesiya akuyamba ulamuliro wake ‘pakati pa adani ake.’ Kuli kokha pambuyo pake kuti iye akuphwanya kotheratu “amitundu,” limodzi ndi mbali iriyonse ya dongosolo loipa la Satana, kukhala losakumbukirikiratu!
Pamene Mesiya Alamulira Dziko Lapansi
14. Kodi nchiyani chimene Mesiya adzakhala wokhoza kuchita atatha kuwononga dongosolo loipa lazinthu la Satana?
14 Itawononga dongosolo la Satana ndi onse olichirikiza, Mfumu Yaumesiyayo, Yesu Kristu, potsirizira pake idzakhala yokhoza kukwaniritsa maulosi odabwitsa Abaibulo amene amafotokoza Ulamuliro wake Wazaka Chikwi. Yesaya 11:1-10 amatithandiza kuwona kuti Mesiyayo adzakhala wolamulira wamtundu wotani. Vesi 2 likutiuza kuti iye adzakhala ndi “mzimu wa Yehova . . . , mzimu wa nzeru ndi wa kuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu.”
15. Kodi ‘mzimu wa mphamvu’ udzatanthauzanji muulamuliro Waumesiya?
15 Talingalirani chimene ‘mzimu wa mphamvu’ udzatanthauza muulamuliro wa Yesu. Pamene iye anali padziko lapansi, anali ndi mlingo wakutiwakuti wa mphamvu yochokera kwa Yehova, yomkhozetsa kuchita zozizwitsa. Ndipo anasonyeza chikhumbo chowona mtima cha kuthandiza anthu, akumati, “Ndifuna.” (Mateyu 8:3) Koma zozizwitsa zake za masiku amenewo zinali kokha kuwonedweratu kwakung’ono kwa zimene anali kudzachita podzalamulira kuchokera kumwamba. Yesu adzachita zozizwitsa pamlingo wa padziko lonse! Anthu odwala, akhungu, ogontha, osalankhula, ndi opunduka adzachiritsidwa kunthaŵi zonse. (Yesaya 35:5, 6) Chakudya chochuluka, chogaŵiridwa bwino lomwe, chidzathetsa njala kosatha. (Salmo 72:16) Bwanji ponena za mamiliyoni osaŵerengeka a awo amene ali m’manda amene Mulungu ali wokondwa kukumbukira? “Mphamvu” za Yesu zidzaphatikizapo mphamvu ya kuwaukitsa, akumapereka kwa aliyense mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso! (Yohane 5:28, 29) Komabe, ngakhale ndi mphamvu yonseyi, Mfumu Yaumesiya nthaŵi zonse idzakhala yodzichepetsa kwambiri. Iyo ikupeza ‘chisangalalo . . . m’kuwopa Yehova.’—Yesaya 11:3.
16. Kodi Mfumu Yaumesiya idzakhala Woweruza wamtundu wanji, ndipo kodi ndimotani mmene zimenezo zidzasiyanira ndi mbiri ya oweruza aumunthu?
16 Mfumu imeneyi idzakhalanso Woweruza wangwiro. Iye “sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera.” Kodi ndiwoweruza waumunthu uti, wa m’nthaŵi yapita kapena wamakono, amene angafotokozedwe mwanjira imeneyo? Ngakhale munthu woweruza bwino kwambiri angathe kuweruza kokha mwa zimene akuwona ndi kumva, mogwiritsira ntchito chidziŵitso chirichonse kapena luntha zimene angakhale ali nazo. Chotero, oweruza ndi aphungu a milandu a dziko lakale lino angasonkhezeredwe kapena kusokonezedwa maganizo ndi umboni wocholowanitsidwa mwaukatswiri, milandu yakalekale ya m’mabwalo amilandu, kapena kusagwirizana kwa umboni. Kaŵirikaŵiri ndiwo olemera kapena amphamvu amene angapeze chitetezo chogwira mtima, kwenikweni mwa kumagula chiweruzo cholungama. Sizidzakhala choncho pansi pa Woweruza Waumesiya! Iye amaŵerenga mitima. Palibe chimene chidzabisika kwa iye. Chiweruzo cholungama, chogwirizanitsidwa ndi chikondi ndi chifundo, sichidzagulitsidwa. Nthaŵi zonse chidzapambana.—Yesaya 11:3-5.
Mmene Ulamuliro Wake Umakuyambukirani
17, 18. (a) Kodi nchithunzithunzi chokongola chotani cha mtsogolo mwa mtundu wa anthu chimene chikusonyezedwa pa Yesaya 11:6-9? (b) Kodi nkwayani kumene ulosi umenewu kwakukulukulu ukugwira ntchito, ndipo kodi nchifukwa ninji ziri choncho? (c) Kodi ndimotani mmene ulosi umenewu udzakhalira ndi kukwaniritsidwanso kwakuthupi?
17 Kaamba ka chifukwa chabwino, ulamuliro wa Mesiya uli ndi chisonkhezero chakuya panzika zake. Umasintha anthu. Yesaya 11:6-9 amasonyeza ukulu wa masinthidwewo. Ulosi umenewu ukupereka chithunzithunzi chogwira mtima cha zinyama zowopsa, zolusa—zimbalangondo, mimbulu, anyalugwe, mikango, mamba—zikumayendera limodzi ndi zinyama zofuyidwa zosavulaza ndipo ngakhale limodzi ndi ana. Koma zolusazo sizikuwopseza konse! Chifukwa ninji? Vesi 9 likuyankha kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”
18 Ndithudi, kukhala “odziŵa Yehova” kungakhale kopanda chiyambukiro chirichonse pazinyama zenizenizo; chotero mavesiŵa ayenera kugwira ntchito kwakukulukulu kwa anthu. Ulamuliro wa Mesiya ukuchirikiza programu ya maphunziro a padziko lonse, kuphunzitsa anthu ponena za Yehova ndi njira zake, kuphunzitsa onse kuchitira anthu anzawo mwachikondi, mwaulemu ndi molemekeza. M’Paradaiso alinkudzayo, Mesiyayo mozizwitsa adzatukulira anthu kuungwiro wakuthupi ndi wamakhalidwe. Zikhoterero zankhalwe, zauchinyama zimene zimaipitsa mkhalidwe wopanda ungwiro waumunthu zidzachoka. Ndiponso, potsirizira pake m’lingaliro lenileni, anthu adzafikira kukhala pamtendere—ndi zinyama!—Yerekezerani ndi Genesis 1:28.
19. Kodi ndimotani mmene ulamuliro wa Mesiya umayambukirira miyoyo ya anthu m’masiku otsiriza ano?
19 Komabe, kumbukirani, kuti Mesiya akulamulira tsopano. Ngakhale tsopano, nzika za Ufumu wake zikuphunzira kukhalira limodzi mumtendere, zikumakwaniritsa Yesaya 11:6-9 m’lingaliro limodzi. Ndiponso, kwazaka pafupifupi 80, Yesu wakhala akukwaniritsa Yesaya 11:10: ‘Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati chizindikiro cha mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.’ Anthu a mtundu uliwonse akutembenukira kwa Mesiya. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chiyambire pamene anayamba kulamulira, iye wakhala ‘akuima monga chizindikiro.’ Wakhala akupangitsa kukhalapo kwake kudziŵidwa kuzungulira padziko lonse mwanjira ya programu yaikulu yamaphunziro yofotokozedwa pamwambapa. Kunena zowona, Yesu ananeneratu kuti ntchito yolalikira ya padziko lonse lapansi ikakhala chizindikiro chachikulu cha kukhalapo kwake mapeto a dongosolo lakaleli lazinthu asanafike.—Mateyu 24:14.
20. Kodi ndilingaliro lotani limene nzika zonse za ulamuliro wa Mesiya ziyenera kupewa, ndipo nchifukwa ninji?
20 Chotero kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu Yaufumu sinkhani yachilendo, yolankhulidwa mwamawu chabe, yongopangira matsutsano a anthu aluntha pakati pa ophunzira zaumulungu. Ulamuliro wake ukuyambukira ndi kusintha miyoyo pano padziko lapansi, monga momwedi Yesaya adaneneratu kuti ukatero. Yesu wapeza mamiliyoni ambiri a nzika zochirikiza Ufumu wake m’dongosolo la dziko loipali. Kodi inu ndinu nzika yoteroyo? Pamenepo tumikiranitu mwachidwi chonse ndi mwachisangalalo zimene Wolamulira wathu akuyenerera! Ndithudi, nkosavuta konse kulema, kugwirizana ndi mfuwu yotonza yadziko yakuti: “Liri kuti lonjezo la kudza kwake?” (2 Petro 3:4) Koma monga momwe Yesu iyemwiniyo adanenera, “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimariziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
21. Kodi ndimotani mmene tonsefe tingakulitsire kuyamikira kwathu chiyembekezo Chaumesiya?
21 Tsiku lirilonse limene likupita limatisendeza pafupi ndi tsiku lalikulu pamene Yehova adzalangiza Mwana Wake kupangitsa kukhalapo kwake kudziŵidwa ndi dziko lonse. Musalole konse chiyembekezo chanu cha tsiku limenelo kufwifwa. Sinkhasinkhani pa za Umesiya wa Yesu ndi za mikhalidwe yake monga Mfumu yolamulira. Lingaliraninso, mwakuya, za Yehova Mulungu, woyambitsa ndi mwini chiyembekezo chachikulu Chaumesiya chofotokozedwa m’Baibulo. Pamene mutero, mosakaikira mudzalingalira mowonjezereka monga momwe mtumwi Paulo anachitira pamene analemba kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!”—Aroma 11:33.
[Mawu a M’munsi]
a Kalelo mu 1864 wodziŵa zaumulungu R. Govett anakulongosola motere: “Zimenezi zikuwonekera kukhala zotsimikizirika kwambiri. Kuperekedwa kwa chizindikiro cha Kukhalapo kumasonyeza kuti nkwachinsinsi. Sitifunikira chizindikiro kuti tidziwe kukhalapo kwa zimene tikuwona.”
b Kaamba ka tsatanetsatane, wonani bukhu lakuti “Let Your Kingdom Come,” tsamba 133-9.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi Kristu akubwerera mumkhalidwe wotani?
◻ Kodi timadziŵa motani kuti pa·rou·siʹa wa Kristu ngwosawoneka ndi wotha nthaŵi yanyengo yaitali?
◻ Kodi ndiliti pamene kukhalapo kwa Kristu kukuyamba, ndipo kodi ndimotani mmene timadziŵira zimenezi?
◻ Kodi Mesiya ali Wolamulira wakumwamba wamtundu wotani?
◻ Kodi ndimnjira zotani m’zimene ulamuliro wa Kristu umayambukira miyoyo ya nzika zake?
[Chithunzi patsamba 15]
Chiyembekezo chakuti Yesu akabweranso chinatanthauza zambiri kwa atumwi ake okhulupirika
[Chithunzi patsamba 17]
Akumalamulira kuchokera kumwamba, Yesu adzachita zozizwitsa pamlingo wa dziko lonse
[Mawu a Chithunzi]
Dziko Lapansi: Chozikidwa pa chithunzithunzi cha NASA