Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/1 tsamba 10-15
  • Kuunikira Chidziŵitso pa Kukhalapo kwa Kristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuunikira Chidziŵitso pa Kukhalapo kwa Kristu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kukhalapo kwa Ambuye Wathu”
  • Chizindikiro
  • Ntchito ya Angelo
  • Chiukiriro Chakumwamba
  • Kulalikira Padziko Lonse
  • Khalani Oyera ndi Opanda Chilema
  • Kudza kwa Yesu Kapena Kukhalapo kwa Yesu—Nchiti?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kristu Alipo!
    Galamukani!—1993
  • Kukhalapo kwa Mesiya ndi Ulamuliro Wake
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kubweranso kwa Kristu
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/1 tsamba 10-15

Kuunikira Chidziŵitso pa Kukhalapo kwa Kristu

“Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, . . . adzalekanitsa [anthu, NW] wina ndi mnzake.”​—MATEYU 25:31, 32.

1. Kodi atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amasulira mawu a pa Mateyu 24:3 kukhala akutanthauza chiyani?

KUTATSALA masiku atatu Yesu asanafe, anayi a ophunzira ake anadza kwa iye namfunsa mwachidwi nati: “Tatiuzani, kodi zinthuzi zidzakhalako liti? ndipo nchiyani chidzakhala chizindikiro cha kubwera [Chigiriki, pa·rou·siʹa] kwanu, ndi cha mapeto a dziko?” Kwa zaka mazana ambiri atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko ndi olemba amasulira mawu ameneŵa onenedwa ndi Yesu pa Mateyu 24:3 (King James Version) kukhala akutanthauza kuti iye akawonekanso m’thupi ndi kuwonedwa ndi mtundu wonse wa anthu. Chifukwa chake, iwo aphunzitsa kuti kubweranso kwa Kristu kukakhala chiwonetsero chachikulu ndi dzoma lowoneka. Amakutcha kubwera kwachiŵiri kwa Kristu. Koma kodi malingaliro awo ngolondola?

2, 3. (a) Kodi nkusiyana kotani kumene Volyumu 2 ya Studies in the Scriptures inasonyeza pakati pa mawu akuti “kubwera” ndi “kukhalapo”? (b) Kodi anthu a Yehova anadzazindikira kuti pa·rou·siʹa ya Kristu imatanthauza chiyani?

2 Podzafika mu 1889, odzozedwa a Yehova, monga onyamula kuunika a m’zaka za zana la 19, anali atawongoleredwa kale pankhani ya kubweranso kwa Kristu. Mu Volyumu 2 ya Studies in the Scriptures, masamba 158 mpaka 161, Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society, analemba kuti: “Parousia . . . imatanthauza kukhalapo, ndipo siiyenera konse kutembenuzidwa kubwera, monga momwe limachitira Baibulo Lachingelezi lofala . . . ‘Emphatic Diaglott,’ matembenuzidwe opindulitsa kwambiri a Chipangano Chatsopano, imamasulira parousia moyenera, kukhalapo . . . , osati kubwera, monga amene ali m’njira, koma kukhalapo, monga wofika kale [Yesu] amati, ‘Monga masiku a Nowa, idzakhalanso tero parousia [kukhalapo] ya Mwana wa munthu.’ Onani kuti kuyerekezerako sikuli pakati pa kubwera kwa Nowa ndi kubwera kwa Ambuye wathu . . . Chotero, kusiyana kuli pakati pa nthaŵi yakukhalapo kwa Nowa pakati pa anthu okhalako ‘chigumula chisanachitike,’ ndi nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu m’dziko, pakubwera kwake kwachiŵiri, ‘moto usanachitike’​—sautso lowopsa la Tsiku la Ambuye [Yehova] lodzetsa mapeto pa mbadwo uno.”​—Mateyu 24:37.

3 Chotero anthu a Yehova a m’zaka za zana la 19 molondola anazindikira kuti pa·rou·siʹa ya Kristu ikakhala yosawoneka. Iwo anazindikiranso kuti mapeto a Nthaŵi za Akunja akafika m’chilimwe cha 1914. Pamene kuunikiridwa kwauzimu kunapitiriza, iwo anadzazindikira kuti Yesu Kristu anaikidwa pampando wachifumu kumwamba monga Mfumu ya Ufumuwo m’chaka chimenecho, 1914.​—Miyambo 4:18; Danieli 7:13, 14; Luka 21:24; Chivumbulutso 11:15.

“Kukhalapo kwa Ambuye Wathu”

4. Kodi “kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Kristu” kumasonya kuchiyani?

4 Chotero, kodi mawu a m’Baibulo akuti “kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Kristu” amatanthauzanji m’tsiku lathu? (1 Atesalonika 5:23, NW) Buku lina limanena kuti liwu lakuti “kukhalapo,” pa·rou·siʹa, “linakhala liwu lalamulo la kuchezera kwa munthu wa malo apamwamba, maka[maka] kwa mafumu ndi olamulira ochezera dera.” Chotero liwuli limasonya ku kukhalapo kwachifumu kwa Ambuye Yesu Kristu monga Mfumu, kuyambira 1914 ndi pambuyo pake, ataikidwa pampando wachifumu kumwamba. Iye alipo mosawoneka ‘akuchita ufumu pakati pa adani ake,’ akulamulira mokangalika monga Mfumu kukwaniritsa lamulo laulosi limeneli. (Salmo 110:2) Kwazaka pafupifupi 79, anthu padziko lapansi awona mphamvu ya kukhalapo kwachifumu kosawoneka kwa Kristu.

5. Kodi nzochitika zotani za mkati mwa pa·rou·siʹa zimene zidzafotokozedwa m’nkhani zitatu zophunzira za magazini ino?

5 Mumpambo uno wa nkhani zitatu, tidzapenda umboni wochititsa chidwi wa zokwaniritsa za Ufumu wa Kristu mkati mwa nyengo imeneyi. Choyamba, tidzasonyeza maulosi angapo Abaibulo amene ananeneratu zochitika zimene zachitika kale kapena ngakhale zimene zikuchitika tsopano. Chachiŵiri, tidzalongosola ntchito yaikulu imene ikuchitidwa ndi kagulu kakapolo wokhulupirika ndi wanzeru kamene Yesu akugwiritsira ntchito m’nyengo yonseyi ya kukhalapo kwake kwachifumu. (Mateyu 24:45-47) Nkhani yachitatu idzatifotokozera chimaliziro chachikulu, nyengo ya “chisautso chachikulu.” Iyo ndiyo nthaŵi imene Yesu adzabwera monga Wakupha wa Yehova kudzawononga anthu osalungama ndi kupulumutsa olungama. (Mateyu 24:21, 29-31) Mtumwi Paulo akufotokoza nthaŵi yachiwonongeko imeneyo kuti idzabweretsa “kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”​—2 Atesalonika 1:7, 8.

Chizindikiro

6. Kodi nchizindikiro chachiungwe chotani chimene chalongosoledwa m’machaputala 24 ndi 25 a Mateyu?

6 Zaka mazana 19 zapitazo, ophunzira a Yesu onyamula kuunika anamfunsa za chizindikiro, kapena umboni, wa kukhalapo kwake kwamtsogolo m’mphamvu yake ya Ufumu. Yankho lake, lolembedwa m’machaputala 24 ndi 25 a Mateyu, limapereka chizindikiro chachiungwe, chimene mbali zake zonse zikukwaniritsidwa tsopano pamlingo wa dziko lonse. Kukwaniritsidwa kwa chizindikirocho kumazindikiritsa nthaŵi ya nsautso ndi chiyeso chachikulu. Yesu anachenjeza kuti: “Yang’anirani, asasokeretse inu munthu. Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhaŵa; pakuti kuyenera kuti izi ziwoneke; koma chitsiriziro sichinafike.”​—Mateyu 24:4-6.

7. Kodi ndimbali ziti za chizindikirocho zimene tawona zikukwaniritsidwa chiyambire 1914?

7 Yesu anapitiriza kulosera kuti padzakhala nkhondo pamlingo waukulu umene sunakhalepo ndi kalelonse. M’kukwaniritsidwa kwake, ziŵiri za nkhondozo zatchedwa nkhondo za dziko, yoyamba kuchokera 1914 mpaka 1918 ndipo yachiŵiri kuchokera 1939 mpaka 1945. Ndiponso, iye anati padzakhala kupereŵera kwa chakudya ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Akristu enieni akazunzidwa kowopsa. Ndendende ndi ulosiwo, Mboni za Yehova, onyamula kuunika amakono, zazunzidwa kwa zaka makumi asanu ndi atatu zapitazo pamene zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu “m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kaamba ka umboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:7-14, NW) Yearbook of Jehovah’s Witnesses iliyonse imawonjezera umboni wakuti mbali zimenezi za chizindikiro zikukwaniritsidwa.

8, 9. (a) Kodi kukhalapo kwachifumu kwa Yesu kumaloŵetsamo chiyani? (b) Kodi ulosi wa Yesu wonena za a Kristu onama umasonyezanji ponena za malo ndi mkhalidwe wa kukhalapo kwake?

8 Popeza kuti ufumu wa Yesu umakuta dziko lonse lapansi, kulambira kowona kukufutukukira ku zigawo zonse za dziko. Kukhalapo (pa·rou·siʹa) kwake kwachifumu kuli nthaŵi ya kuyang’anira kwa padziko lonse. (1 Petro 2:12) Koma kodi pali mzinda walikulu, kapena malo apakati, kumene anthu angamfikire Yesu ndi zofunsa zawo? Yesu anayankha funsoli mwakuneneratu kuti poyembekezera kukhalapo kwake, padzauka a Kristu onama. Anachenjeza kuti: “Akanena kwa inu, Onani, iye [Kristu] ali m’chipululu; musamukeko. Onani, ali m’zipinda; musavomereze. Pakuti monga mphezi idzera kum’maŵa, niwonekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake kwa Mwana wa munthu.”​—Mateyu 24:24, 26, 27.

9 Kuposa wina aliyense padziko lapansi, Yesu, “Mwana wa munthu,” anadziŵa kumene akakhala pamene kukhalapo kwake kukayamba. Iye sakakhala kuno kapena kuja kapena m’malo aliwonse padziko lapansi. Iye sakawonekera kumalo akutali, “m’chipululu,” kuti awo ofunafuna Mesiya akakambirane naye ali kutaliko osawonedwa ndi akuluakulu a boma la dzikolo, kumalo amene otsatira ake akaphunzitsidwa naye, akumakonzekera kuukira boma ndi kukhazikitsa iye monga Wolamulira wa dziko Waumesiya. Ndiponso, iye sakabisala “m’zipinda,” ndipo malo akewo nkukhala odziŵika kwa osankhidwa oŵerengeka okha, ndi kuti kumeneko, mosawoneka ndi mosadziŵika ndi aliyense, akapanga ndi kulinganiza chiŵembu mwamtseri ndi omtsatira ake kuti agwetse maboma a dzikoli ndiyeno nkukhala paulamuliro monga Mesiya wolonjezedwayo. Kutalitali!

10. Kodi ndimotani mmene mphezi za chowonadi cha Baibulo zang’animira kuŵalira dziko lonse lapansi?

10 Mosiyana nzimenezo, sipakakhala kubisa kulikonse pakufika kwa Yesu monga Mfumu, pakuyambika kwa kukhalapo kwake kwachifumu. Monga momwe Yesu ananeneratu, pamlingo wadziko lonse, mphezi za chowonadi cha Baibulo zikupitirizabe kung’anima moŵalira madera aakulu kuchokera ku mbali zakum’maŵa mpaka ku mbali zakumadzulo. Ndithudi, monga onyamula kuunika amakono, Mboni za Yehova zikutsimikizira kukhala “kuunika kwa amitundu, kuti . . . chipulumutso [cha Yehova chifike] ku malekezero a dziko lapansi.”​—Yesaya 49:6.

Ntchito ya Angelo

11. (a) Kodi ndimnjira yotani mu imene makamu a angelo amagwiritsiridwa ntchito kuŵalitsa kuunika kwa Ufumu? (b) Kodi nliti pamene ziŵalo za tirigu zasonkhanitsidwa ndipo m’gulu liti?

11 Malemba ena onena za kukhalapo kwa Yesu amamfotokoza kukhala ali pamodzi ndi makamu a angelo, kapena ‘akuwatumiza.’ (Mateyu 16:27; 24:31) M’fanizo la tirigu ndi namsongole, Yesu ananena kuti “munda ndiwo dziko lapansi” ndipo “kututa ndicho chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.” Komabe, izi sizitanthauza kuti mkati mwakukhalapo kwake m’mphamvu ndi ulemerero wa Ufumu wake, iye akugwiritsira ntchito angelo amithenga okha pa ntchito zapadziko lapansi. Kuyambira mu 1919, angelo motsogozedwa ndi Yesu analekanitsa gulu la tirigu la odzozedwa obadwa ndi mzimu okhala padziko lapansi, amene anabalalitsidwa ndi zochitika za Nkhondo Yadziko I, ndipo iwoŵa anakonzekeretsedwa kaamba ka ntchito yowonjezereka m’dzina la Mfumuyo. (Mateyu 13:38-43) M’ma 1920 zikwi zina za anthu zinaima kumbali ya Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa ndipo zinadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Odzozedwa ameneŵa mokangalika anagwirizana ndi otsalira oyambirirawo. Onse pamodzi, amapanga kagulu kakapolo wokhulupirika ndi wanzeru wa m’tsiku lathu.

12. Kodi ndikuyeretsa kotani kumene angelo akhalamo ndi phande, ndipo ndi chotulukapo chotani ku dziko lapansi?

12 Chitsanzo china cha kukhalamo ndi phande kwa angelo mkati mwa kukhalapo kwa Yesu ataikidwa pampando wake wachifumu mu 1914 chinalembedwa pa Chivumbulutso 12:7-9 kuti: “Mikayeli [Yesu Kristu] ndi angelo ake a[na]chita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Motero, miyamba tsopano njoyeretsedwa, kwangotsala malo apadziko lapansi a Ufumuwo kuti ayeretsedwe kotheratu kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. M’chaka chino cha 1993, chenjezo laumulungu likugwirabe ntchito lakuti: “Tsoka mtunda . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”​—Chivumbulutso 12:12.

Chiukiriro Chakumwamba

13, 14. (a) Kodi Malemba amasonyeza kuti nchiyani chimene chakhala chikupitiriza kuyambira 1918 kumkabe mtsogolo? (b) Kodi Paulo ndi Yohane akuvumbulanji ponena za odzozedwa lerolino?

13 Chochitika china chochititsa chidwi mkati mwa kukhalapo kwa Kristu ndicho kuyambika kwa chiukiriro chakumwamba. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti Akristu odzozedwa amene anagona kalelo m’manda awo adzakhala oyamba kuuka ndi kukhala ndi Kristu Yesu m’malo auzimu. Umboni waperekedwa kwa zaka zambiri wosonyeza kuti zimenezi zinachitika kuyambira 1918 kumka mtsogolo. Paulo analemba kuti: “Mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo. Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Kristu; pomwepo iwo a Kristu, pa [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake.” (1 Akorinto 15:22, 23) Chiukiriro cha odzozedwa mkati mwa kukhalapo kwa Kristu chimatsimikiziridwa pa 1 Atesalonika 4:15-17 kuti: “Ichi tinena kwa inu m’mawu a [Yehova, NW], kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti . . . akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga.” Pali odzozedwa 144,000 amene ali a Kristu amene pomalizira pake adzalandira mphotho yodabwitsa imeneyi.​—Chivumbulutso 14:1.

14 Monga momwe Paulo akusonyezera, otsalira odzozedwa amenewo okhala ndi moyo lerolino samaloŵa mu Ufumuwo asanatero Akristu odzozedwa oyambirira ofera chikhulupiriro ndi ophunzirawo. Mtumwi Yohane akufotokozanso za odzozedwa amene amafa lero motere: “Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi,” ndiko kuti, m’kukhalapo kwawo ataukitsidwa. (Chivumbulutso 14:13) Ndipo Paulo akuti: “Tawonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse [mu imfa, NW], koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.” (1 Akorinto 15:51, 52) Ha, nchozizwitsa chodabwitsa chotani nanga!

15, 16. (a) Kodi ndifanizo lotani limene Yesu anapereka pa Luka 19:11-15, ndipo ndi chifukwa chotani? (b) Kodi ulosi umenewu wakhala ukukwaniritsidwa motani?

15 Nthaŵi ina pamene Yesu anali kulalikira kwa gulu la otsatira ake za Ufumu wa Mulungu, anagwiritsira ntchito fanizo kuwathandiza kuwongolera malingaliro awo olakwa. Nkhaniyo imati: “Iwo anayesa kuti ufumu wa Mulungu ukuti uwonekere pomwepo. Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka anamka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. . . . Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziŵe umo anapindulira pochita malonda.”​—Luka 19:11-15.

16 Yesu anali ‘munthuyo’ amene anapita kumwamba, “dziko lakutali” kumene anakalandira ufumu. Ufumuwo anaulandira mu 1914. Posapita nthaŵi, Kristu monga Mfumu anachita kuŵerengera ndi odzinenera kukhala otsatira ake kuwona zimene anachita m’kusamalira zabwino za Ufumu zimene anawaikizira. Okhulupirika oŵerengeka anasankhidwa kuti alandire chiyamikiro cha mbuye wawo kuti: “Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m’chaching’onong’ono, khala nawo ulamuliro pa midzi khumi.” (Luka 19:17) Nyengo imeneyi ya kukhalapo kwa Kristu inaloŵetsamo ntchito yaikulu ya kulalikira mbiri ya Ufumu, kuphatikizapo kulengezedwa kwa ziweruzo za Mulungu pa oipa, ndipo kuyang’anira ntchitoyi kunaphatikizidwa muulamuliro wopatsidwa kwa “kapolo wabwino” ameneyo.

Kulalikira Padziko Lonse

17. Kodi nchisangalalo chotani chimene chikukhalapo mkati mwa pa·rou·siʹa?

17 Kodi nchiyani china chikachitika mkati mwa pa·rou·siʹa? Ikakhala nthaŵi ya chisangalalo chachikulu m’ntchito yakulalikira ndi kuthandiza atsopano kukonzekera chipulumutso kupyola chisautso chachikulu chilinkudza. Iwoŵa a “khamu lalikulu,” amene akuthandiza otsalira, amakhala ‘makalata achivomerezo.’ (Chivumbulutso 7:9; 2 Akorinto 3:1-3) Paulo akutchula chisangalalo cha ntchito yakututa imeneyi pamene akunena kuti: “Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? sindinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu [m’kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake?”​—1 Atesalonika 2:19.

Khalani Oyera ndi Opanda Chilema

18. (a) Kodi ndipemphero la Paulo lotani limene limanena za pa·rou·siʹa? (b) Kodi ndimzimu wotani umene tonsefe tiyenera kusonyeza m’nthaŵi ino, ndipo mwanjira zotani?

18 Paulo anapemphereranso kuyeretsedwa kwa awo okhala m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu kuti: “Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kukhalapo [pa·rou·siʹa] kwake kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Atesalonika 5:23) Inde, lerolino, kaya ndife otsalira odzozedwa kapena a chiŵerengero chachikulu cha nkhosa zina, mzimu wachigwirizano umatimangirira pamodzi mokhulupirika kuti tipitirize kukhala oyera ndi opanda chilema panthaŵi ino yapadera. Mofananamo, tiyenera kukhala oleza mtima. Yakobo anati: “Lezani mtima, abale, kufikira [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake kwa Ambuye. . . . Limbitsani mitima yanu; pakuti [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake kwa Ambuye kuyandikira.”​—Yakobo 5:7, 8.

19. Kodi Petro anapereka chenjezo lotani ponena za pa·rou·siʹa, ndipo kodi tiyenera kuchitaponji?

19 Mtumwi Petro analinso ndi chonena kwa ife amene tikukhala m’nyengo ino. Anatichenjeza za onyoza, amene alipo ambiri m’mbali zonse za dziko lapansi. Petro akuti: “Kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la [kukhalapo (pa·rou·siʹa)] kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” (2 Petro 3:3, 4) Chinkana kuti pali onyoza ochuluka mkati mwa kukhalapo kwa Kristu, anthu a Yehova akupitiriza kuŵala monga kuunika kwa dziko, kaamba ka chipulumutso cha ambiri.

Mafunso Akubwereramo

◻ Kodi anthu a Yehova anapitiriza motani kuunikiridwa ponena za pa·rou·siʹa?

◻ Kodi lemba la Mateyu 24:4-8 lakhala likukwaniritsidwa motani?

◻ Kodi angelo akhala akugwirizana motani ndi Kristu wokhazikitsidwa pampando wachifumu?

◻ Kodi nchozizwitsa chodabwitsa chotani chimene chikuwoneka kukhala chikuchi- tikira pamodzi ndi pa·rou·siʹa?

◻ Kodi nchisangalalo chotani chimene chilipo m’nthaŵi ino, ndipo ndani akukhala nacho?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena