Njira Zosiyanasiyana Zogawirira Magazini Akale
Si bwino kungosunga kapena kutaya magazini akale chifukwa kuchita zimenezi kungachititse kuti asathandize aliyense. Tiyenera kuyesetsa kugawira magazini amenewa. Ngakhale magazini imodzi, ikhoza kuthandiza munthu kukhala ndi chidwi chofuna kuphunzira choonadi n’kuyamba kuitanira pa dzina la Yehova. (Aroma 10:13, 14) Mungagawire magaziniwa pogwiritsa ntchito njira zotsatirazi:
Mukamalalikira m’gawo loti sililalikiridwa kawirikawiri, ndipo mwafika pakhomo poti palibe anthu, mwina mungasiye magaziniwo pamalo oti eninyumba adzathe kuwaona.
Mukamalalikira m’malo opezeka anthu ambiri monga pasiteji kapena pasiteshoni ya sitima, funsani anthu ngati angafune chinachake choti aziwerenga. Ndiyeno asonyezeni magazini akale angapo kuti asankhepo amene angakonde kuwerenga.
Mukapita kumalo monga kusukulu, kulaibulale kapena kuchipatala, mungasiye magazini angapo pamalo odikirira. Koma ndi bwino kupempha kaye chilolezo musanachite zimenezi. Komanso ngati mwapeza kuti pali kale magazini athu, si bwino kusiyanso ena.
Pokonzekera maulendo obwereza, ganizirani za munthu aliyense amene mukufuna kukakumana naye. Kodi ali pabanja? Kodi amayendayenda? Kapena amakonda kudzala maluwa pakhomo? Fufuzani m’magazini akale kuti mupeze nkhani imene angasangalale nayo, n’kukamusonyeza.
Ngati mwapeza munthu wachidwi amene mwakhala mukupita pakhomo lake maulendo angapo koma osam’peza, musonyezeni magazini angapo amene munali musanam’patse.