“Gawirani Magazini Kapena Kabuku Kakale Kogwirizana Ndi Zimene Munthu Alinazo Chidwi”
Mwina mwaona kuti m’miyezi imene tikuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ngati mwini nyumba ali nalo kale bukuli ndipo sakufuna kuti muziphunzira naye Baibulo, tikulimbikitsidwa kumugawira magazini kapena kabuku kakale kamene kakugwirizana ndi zimene munthuyo ali nazo chidwi. N’chifukwa chiyani zili choncho?
N’chifukwa chakuti timabuku komanso magazini akale amakhala ndi nkhani zogwirizana kwambiri ndi zimene anthu ali nazo chidwi. N’kutheka kuti nkhani inayake m’mabuku amenewa ingamukhudze mtima kwambiri mwininyumba. Choncho, mukamaika mabuku m’chikwama chanu cha mu utumiki, onetsetsani kuti mwaikamo timabuku tosiyanasiyana komanso magazini akale. Ngati mulibe magazini akale, mwina mungapeze ku Nyumba ya Ufumu ngati alipo. Ndiyeno ngati mwininyumba ali nalo kale buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo sakufuna kuti muziphunzira naye Baibulo, mungamuonetse magazini kapena timabuku timeneti n’kumuuza kuti atenge timene akufuna. Mukatero, konzani zodzamuyenderanso kuti mukulitse chidwi chake. Mwina pa mapeto pake akhoza kudzalola kuti muziphunzira naye Baibulo.