Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/12 tsamba 2-3
  • Thandizani Anthu Kumvera Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Anthu Kumvera Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Mverani Mulungu?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Mabrosha—Zipangizo za Muutumiki Zamtengo Wapatali
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 7/12 tsamba 2-3

Thandizani Anthu Kumvera Mulungu

1. Kodi pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Ufumu wa Mulungu Ubwere,” panatulutsidwa timabuku tanji, ndipo n’chifukwa chiyani timabuku timeneti tili tothandiza kwambiri?

1 Pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Ufumu wa Mulungu Ubwere,” panatulutsidwa timabuku tiwiri, kamodzi kanali ndi mutu wakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo kena kanali kakuti Mverani Mulungu. Chifukwa chakuti timabukuti tilibe mawu ambiri, n’tosavuta kumasulira moti pamene kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kankatulutsidwa kanali katavomerezedwa kuti kamasuliridwe m’zinenero 431.

2. Kodi ndani amene angapindule kwambiri ndi timabuku timeneti?

2 Kodi ndani amene apindule kwambiri ndi timabuku timeneti? Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza nthawi imene mungagwiritse ntchito timabukuti:

• Wofalitsa akukambirana ndi mwininyumba, paulendo woyamba kapena paulendo wobwereza, ndipo wazindikira kuti mwininyumbayo sadziwa kuwerenga kapena amawerenga movutikira.

• Wofalitsa akulalikira kwa anthu amene amalankhula chinenero chomwe chili ndi mabuku athu ochepa kapena chilibiretu. Kapena ambiri m’deralo satha kuwerenga chinenero chimene amalankhula.

• Wofalitsa akulalikira munthu wogontha m’chinenero cha manja.

• Kholo likufuna kuphunzitsa choonadi mwana wake wamng’ono yemwe sanayambe kuwerenga.

3. Kodi kabuku kakuti Mverani Mulungu kanakonzedwa bwanji?

3 Mmene Timabukuti Tinapangidwira: Kabuku kakuti Mverani Mulungu kalibe mawu ambiri. M’munsi mwa tsamba lililonse mumakhala chiganizo chachifupi chofotokoza mfundo yaikulu ndi lemba lake. N’chifukwa chiyani kanalembedwa chonchi? Kuti timvetse, tiyerekeze kuti munthu winawake wakupatsani kabuku ka m’chinenero chomwe inuyo simutha kuwerenga ndipo zilembo zake n’zachilendo. Kodi mungafune kukawerenga ngakhale katakhala ndi zithunzi zokongola? Anthu ambiri sangafune kukawerenga. Ndi mmenenso zimakhalira ndi anthu osatha kuwerenga, iwo amagwa ulesi akapatsidwa buku limene lili ndi mawu ambirimbiri. Chifukwa cha zimenezi, tsamba lililonse la kabukuka lili ndi zithunzi zokhala ndi chizindikiro cholozera chithunzi chotsatira.

4. Kodi kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kanakonzedwa bwanji?

4 Zithunzi zomwe zili m’kabuku kakuti Mverani Mulungu ndi zofanana ndi zithunzi zomwe zili m’kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Kabukuka kanapangidwa kuti kazigwiritsidwa ntchito kuphunzira ndi anthu omwe amawerenga movutikira kapena amene satha kuwerenga n’komwe. Munthu amene akuchititsa phunziro pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu akhozanso kugwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kuti apeze mfundo zofotokozera zithunzi. Mutu uliwonse anaulemba ngati funso ndipo mayankho ake amapezeka m’nkhaniyo. Chithunzi chilichonse chili ndi mawu ofotokozera komanso malemba. M’munsi mwa masamba ena muli kabokosi kokhala ndi mfundo zoonjezera komanso malemba amene mungakambirane ndi wophunzirayo, ngati mukuona kuti n’zofunika kutero.

5. Kodi mungagawire timabukuti pa nthawi iti?

5 Mmene Mungagwiritsire Ntchito Timabukuti: Mungagawire timabukuti polalikira nyumba ndi nyumba nthawi ina iliyonse imene mukuona kuti m’pofunika kutero, ngakhale kuti simukugawira timabuku m’mwezi umenewo. (Onani bokosi lakuti, “Zimene Munganene Pogawira Timabukuti.”) Mukhozanso kugawira kabukuka pa ulendo wobwereza. Mungamuuze munthuyo kuti ulendo uno mwamubweretsera kabuku kena, kenako mungamupatse.

6. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji timabuku timeneti popangitsa phunziro la Baibulo?

6 Kabuku kakuti Mverani Mulungu kalibe mafunso oti mungagwiritse ntchito pophunzira ngati mmene mumachitira pophunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Anthu ambiri amakonda kumvetsera wina akamakamba nkhani inayake. Choncho muzigwiritsa ntchito zithunzi pofotokoza nkhani za m’Baibulo ndipo fotokozani mfundo ya chithunzi chilichonse. Muzisonyeza kuti nkhaniyo ikukusangalatsani ndipo muzimuuza wophunzira wanu kuti afotokoze zimene akuona. Muziwerenganso malemba amene ali m’munsi mwa tsamba lililonse ndipo mudzikambirana zimene malembawo akutanthauza. Muzimufunsa mafunso kuti azinena maganizo ake komanso kuti mudziwe kuti akumvetsa zimene mukukambirana. Ngati mukugwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, werengani mfundo zowonjezera komanso malemba pokambirana chithunzi chilichonse.

7. Kodi tingathandize bwanji anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo kuti apite patsogolo?

7 Thandizani Wophunzira Wanu Kupita Patsogolo: Tikukhulupirira kuti zimene mungamakambirane ndi munthu amene mukuphunzira naye Baibulo, zingamuthandize kuti akhale ndi chidwi chophunzira kuwerenga n’cholinga choti azitha kuphunzira za Yehova payekha. (Mat. 5:3; Yoh. 17:3) Choncho, ngati mukukambirana naye kabuku kakuti Mverani Mulungu, pakapita nthawi mungayambe kumuphunzitsa kuwerenga kenako mungadzayambe kukambirana kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Sikuti mukadzamaliza kukambirana naye timabukuti ndiye kuti wophunzirayo akhoza kubatizidwa. Muyeneranso kuphunzira naye buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena buku lina loyenerera limene lingamuthandize kumvetsa bwino Baibulo.

8. N’chifukwa chiyani mukuthokoza Mulungu chifukwa chotipatsa timabuku tatsopano togwiritsira ntchito mu utumiki?

8 Anthu ayenera kumvera Wolamulira Wamkulu kuti adzakhale ndi moyo wosatha. (Yes. 55:3) Ndipo Yehova akufuna kuti anthu “kaya akhale a mtundu wotani,” kuphatikizapo osatha kuwerenga, azimumvera. (1 Tim. 2:3, 4) Tikuyamikira kwambiri kuti tili ndi timabuku tatsopano timeneti, tomwe tingagwiritse ntchito pothandiza anthu kuti azimvera Mulungu.

[Bokosi patsamba 3]

Zimene Munganene Pogawira Timabukuti

Muonetseni mwininyumba zithunzi za patsamba 2 ndi 3 kenako mufunseni kuti: “Kodi mungakonde kudzakhala m’dziko lotereli? [Yembekezani ayankhe.] Malemba amalonjeza [kapena munganene kuti, buku loyera ili limalonjeza] kuti Mulungu adzasintha dzikoli kuti likhale lokongola, lamtendere ndipo sikudzakhalanso matenda kapena umphawi. Taonani zimene tiyenera kuchita kuti tidzakhale m’dziko limenelo. [Werengani lemba la Yesaya 55:3, lomwe lili pamwamba pa tsamba 3.] Lembali likutiuza kuti tiyenera ‘kupita’ kwa Mulungu komanso ‘kumumvera.’ Koma kodi tingatani kuti tizimvera Mulungu?” Pitani patsamba 4 ndi 5 ndipo kambiranani zithunzi komanso malemba kuti mupeze yankho la funso limeneli. Ngati alibe nthawi, mukhoza kumusiyira kabukuko, n’kupangana zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane yankho la funso limeneli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena