Ndandanda ya Mlungu wa July 16
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 16
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero
❑ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 9 ndime 1-7 ndi mabokosi a patsamba 68 ndi 70 (Mph. 25)
❑ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 15–17 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 16:14-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Choonadi Chimene Yesu Ankanena pa Yohane 18:37 N’chiyani? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yesu Ndi Amene Anayambitsa Mwambo wa Misa?—rs tsa. 282 ndime 4 mpaka tsa. 284 ndime 4 (Mph. 5)
❑ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu Ikuthandizeni Kupita Patsogolo Mwauzimu. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira Sukulu ya Utumiki, yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 6 ndime 1 mpaka kumapeto kwa tsamba 8. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti afotokoze mmene sukuluyi yawathandizira mu utumiki.
Mph. 20: “Thandizani Anthu Kumvera Mulungu.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime yachisanu, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire kamodzi ka timabuku tathu. Mukamaliza kukambirana ndime 6, chitani chitsanzo cha mphindi zitatu chosonyeza wofalitsa akuchititsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti, Mverani Mulungu ndipo akambirane zithunzi za patsamba 4.
Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero