Mabrosha—Zipangizo za Muutumiki Zamtengo Wapatali
1 Kaŵirikaŵiri mmisiri waluso amanyamula zipangizo zosiyanasiyana, chilichonse chimakhala ndi ntchito yake. Monga olengeza Ufumu, tili ndi mabrosha osiyanasiyana ambiri amene angatithandize kukwaniritsa mwaluso zosoŵa zauzimu za anthu amene timawalalikira. (Miy. 22:29) Pakhomo limodzi mungakumane ndi wina amene ali wopsinjika maganizo. Pena, mwininyumba amene akulakalaka boma lodalirika, pamene wina wake akukayikira ngati moyo uli ndi chifuno chilichonse. Kodi ndimotani mmene tingagwiritsirire ntchito mabrosha athu kuthandiza anthuwa?
2 Pogaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?,” mukhoza kunena zonga izi:
◼ “Anthu ena amene amaona kuvutika ndi chisalungamo m’dziko amakonda kuimba Mulungu mlandu wa zonsezi. Amalingalira kuti popeza kuti Mulungu ali wamphamvuyonse, iye akanathetsa kuvutika kwathu ngati amatisamaliradi. Kodi muganiza bwanji pa zimenezi? [Yembekezerani yankho.] Salmo 72:12-14 limasonyeza kuti Mulungu amatisamaliradi. Kuvutika ndi chisalungamo sizili mlandu wake. Iye walonjeza kuti ochita zoipa adzachotsedwa posachedwa. Brosha ili lakuti, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, limasonyeza zimene adzachita ndi mmene ife tingapindulire.” Mwina mungakhoze kupitiriza kukambitsirana mwa kugwiritsira ntchito ndemanga zimene zili patsamba 27, ndime 22.
3 Ngati mukugwiritsira ntchito brosha lakuti “Chifuno cha Moyo,” mungafune kuyamba motere:
◼ “Ndithudi, pafupifupi munthu aliyense amafuna kudziŵa chifuno cha moyo. Kodi ndicho kungokhala zaka 70 kapena 80 ndiyeno kumwalira? Kapena kodi moyo uli ndi zambiri? Muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Panopa pa Salmo 37:29, timapezapo chifuno chabwino koposa cha Mulungu kaamba ka munthu ndi dziko lapansi.” Mutaŵerenga lembalo, tsegulani pachithunzithunzi cha patsamba 31, ndi kupereka ndemanga zowonjezereka ponena za mmene kukhala ndi moyo m’Paradaiso kudzakhalira.
4 Brosha lakuti “Tawonani!” lingagaŵiridwe mwa kusonyeza chithunzithunzi chonse cha pachikuto ndi kufunsa kuti:
◼ “Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chingafunikire kuti dziko lapansi lioneke moteremu? [Yembekezerani yankho.] Aliyense pachithunzithunzichi ali ndi nyumba ndi ntchito yosangalatsa. Pali mtendere ndi zakudya zochuluka, ndipo dziko lapansi nlosaipitsidwa. Mulimonse mmene maboma aumunthu angayesere, nkosatheka kwa iwo kudzetsa dziko lotere. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu ‘adzachita zonse kuti zikhale zatsopano.’ [Tsegulani patsamba 30, ndipo ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Brosha limeneli lingakuthandizeni kuphunzira zimene mufunikira kuchita kuti mukakhale m’dziko latsopano limenelo.” Ngati chikondwerero chachikulu chasonyezedwa, tsegulani patsamba 3, ndi kusonyeza mmene timachitira phunziro la Baibulo.
5 Mwina mungagwiritsire ntchito njira yotsatirayi ndi brosha lakuti “Moyo pa Dziko Lapansi”:
◼ “Anthu ambiri amaganiza kuti adzafunikira kupita kumwamba kuti akasangalale ndi moyo wosatha, koma kodi muganiza bwanji ponena za kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatitsimikizira kuti moyo wamuyaya uli wotheka, ndipo limatiuza mmene tingafikire chonulirapo chimenecho.” Ŵerengani Yohane 17:3. Ndiyeno sonyezani mwininyumbayo chithunzithunzi 49, ndi kufunsa kuti: “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo m’dziko longa ili?” Gaŵirani broshalo, ndipo pangani makonzedwe a ulendo wobwereza.
6 Mabroshawo ali ndi nkhani zapanthaŵi yake, amayankha mafunso a anthu, ndi kupereka chitonthozo. Mwa kugwiritsira ntchito zipangizo zimenezi mwaluso, tingathandize oona mtima kuti “afike pozindikira choonadi.”—1 Tim. 2:4.