Khalani Aphunzitsi a Mawu a Mulungu—Mwa Kugwiritsira Ntchito Mabrosha
1 Mtumiki wa Yehova aliyense wodzipatulira ali ndi thayo la kukhala ndi phande m’ntchito yophunzitsa ena Mawu a Mulungu. Ukulu wa thayo limeneli umaonekera bwino pamene tizindikira kuti amene watipatsa ntchito ya “kupanga ophunzira a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa,” ndi uyo amene ali ndi ulamuliro kumwamba ndi pa dziko lapansi. (Mateyu 28:18-20, NW ) Chotero, kukhala ndi phande m’kulalikira uthenga wabwino kumafuna kuti tikhale aphunzitsi!—2 Tim. 2:2.
2 Mu August tingagwiritsire ntchito maluso athu a kuphunzitsa pogaŵira mabrosha. Tingasankhulemo malingaliro okondweretsa a m’Malemba ndi kukonzekera ndemanga zingapo zimene zidzatithandiza kuyambitsa makambitsirano.
3 Pogaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” munganene kuti:
◼ “Tafikira anansi anu ambiri ndipo tapeza kuti ali odera nkhaŵa kwambiri ponena za kuwonjezeka kwa upandu, uchigaŵenga, ndi chiwawa. Kodi inu muganiza kuti nchiyani chimene chachititsa zimenezi kukhala vuto lalikulu motere? [Yembekezerani yankho.] Nzochititsa chidwi kwambiri kwa ife kuona kuti Baibulo lidaneneratu kuti zimenezi zidzachitika. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1-3.] Onani kuti zimenezi ziyenera kuchitika mu ‘masiku otsiriza.’ Zimenezi zikutanthauza kuti chinthu chinachake chikufika kumapeto ake. Kodi muganiza nchiyani chimenecho?” Yembekezerani yankho. Tsegulani patsamba 22, sonyezani chithunzithunzicho, ndi kukambitsirana lemba limodzi kapena aŵiri ogwidwa mawu patsamba limenelo. Pangani makonzedwe akudzabweranso kudzafotokoza chifukwa chake timakhulupirira kuti madalitso ameneŵa ali pafupi.
4 Mwina mungafune kugwiritsira ntchito kafikidwe aka pogaŵira brosha lakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?”:
◼ “Anthu ambiri akukhala ndi vuto kuti adziŵe chifuno chenicheni chokhalira ndi moyo. Ngakhale kuti anthu ena ali achimwemwe pang’ono, ochuluka akukhala ndi moyo wodzala ndi zogwiritsa mwala ndi kuvutika. Kodi muganiza kuti ndiwo moyo umene Mulungu anafuna kuti tikhale nawo? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akufuna kuti tikhale m’dziko longa ili.” Sonyezani chithunzithunzi cha patsamba 21, ndiyeno tsegulani patsamba 25 ndi 26, ndime 4-6, ndi kulongosola zimene walonjeza. Funsani funso ili loti mudzakambitsirane pamene mubweranso: “Kodi tingatsimikize motani kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake?”
5 Mungagaŵire brosha lakuti “Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!” mwa kusonyeza chithunzithunzi chonse pa chikuto chakumaso ndi chakumbuyo ndi kufunsa kuti:
◼ “Kodi mungakonde kukhala m’dziko la anthu achimwemwe okhaokha monga pano? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatiuza kuti Mulungu amakonda anthu ndipo amafuna kuti akhale ndi moyo kosatha mwachimwemwe pa dziko lapansi lino.” Tsegulani pa chithunzithunzi 49, ndi kuŵerenga limodzi la Malemba osonyezedwa. Ndiyeno sonyezani chithunzithunzi 50, ndi kulongosola zimene tiyenera kuchita ngati tifuna kukhala m’Paradaiso ameneyu. Lonjezani kuti mudzabweranso kudzakambitsirana chifukwa chake chikhulupiriro mwa Yesu Kristu chili chofunika kwambiri.
6 Yehova amakondwera pamene tichititsa ‘kukula kwathu kuonekera mwa kudzipenyerera ndi chiphunzitso chathu.’ (1 Tim. 4:15, 16) Mabrosha athu angakhale thandizo lenileni kwa ife pakuyesayesa kwathu kuthandiza amene amalakalaka kumva “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Yes. 52:7.