Ndandanda ya Mlungu wa March 31
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 31
Nyimbo Na. 70 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 9 ndime 14-19 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 2:1-14 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kubweranso kwa Khristu Kudzakhala Kosaoneka—rs tsa. 162 ndime 3–tsa. 163 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kutsutsana ndi Anthu Osankhidwa Ndi Mulungu Kuli Ngati Kutsutsana Ndi Yehova—lv tsa. 43-44 ndime 15-17 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Njira Zosiyanasiyana Zogawirira Magazini Akale.” Nkhani yokambirana. Dziwitsani mpingo za magazini akale amene alipo oti ofalitsa angathe kukagawira mu utumiki. Pemphani omvera kuti afotokoze zosangalatsa zomwe zinachitika atagawira magazini akale. Pomaliza, funsani woyang’anira utumiki kuti afotokoze mmene ntchito yogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso ikuyendera.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 28:20 komanso 2 Timoteyo 4:17. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero