Ndandanda ya Mlungu wa March 24
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 24
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 9 ndime 8-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 47-50 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 48:17-22 ndi 49:1-7 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zochitika Zosonyeza Kukhalapo kwa Khristu Zimatenga Nyengo ya Zaka Zambiri—rs tsa. 162 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: Kudzikuza Kumabweretsera Mavuto—Miy. 11:2; 1 Pet. 5:5-7 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Tsanzirani Nehemiya. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene chitsanzo cha Nehemiya chingatithandizire pa ntchito yathu yolalikira.
Mph. 10: Muzigwiritsa Ntchito Mafunso Kuti Muziphunzitsa Mogwira Mtima—Gawo 1. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 236 mpaka 237 ndime 2. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mfundo imodzi ya m’nkhaniyi.
Mph. 10: Yehova Amamva Pembedzero la Anthu Olungama. (1 Pet. 3:12) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2013, tsamba 66 ndime 1 mpaka 3 komanso tsamba 104 ndi 105. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero