Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Chaka chatha, anthu 289,499 anabwera pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Khristu. Chiwerengerochi ndi chowirikiza katatu chiwerengero cha Mboni za Yehova m’Malawi muno. Tiyeni tiyesetse kuitananso anthu ambiri chaka chino kuti adzabwere pa Chikumbutso, chomwe chidzachitike pa 3 April. Anthuwa adzaphunzira za chikondi chimene Mulungu anatisonyeza anthufe komanso zimene Mulungu watilonjeza.—Yoh. 3:16.