Ndandanda ya Mlungu wa March 9
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 9
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 9 ndime 21-24 ndi bokosi patsamba 96 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 1-4 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 2:30-36 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Kodi Baibulo Linaneneratu Zinthu Ziti Zokhudza Mesiya?—igw tsa. 10 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tikudziwa Bwanji Kuti Mulungu Amayankha Mapemphero?—bt tsa. 69-70 ndime 4-7 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Khalani Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Mph. 10: ‘Khalani Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’ Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. Werengani ndi kukambirana malemba otsatirawa: Miyambo 21:5, Tito 3:1, ndi 1 Petulo 3:15. Fotokozani chifukwa chake kukonzekera n’kofunika kwa Akhristufe. Fotokozaninso mwachidule nkhani zina za m’Msonkhano wa Utumiki za mwezi uno. Mufotokozenso mmene nkhanizo zikugwirizanirana ndi mutu wa mwezi uno.
Mph. 10: Funsani Woyang’anira Sukulu. Kodi ntchito yanu ndi yotani? Kodi mumakonzekera bwanji kuchititsa sukulu mlungu uliwonse? N’chifukwa chiyani aliyense yemwe ali ndi nkhani m’Sukulu ya Utumiki ayenera kukonzekera bwino? Kodi aliyense angapindule bwanji ngati atawerengeratu malifalensi a nkhani zomwe zikambidwe, asanabwere kumisonkhano?
Mph. 10: “Kodi Mwayamba Kukonzekera Chikumbutso?” Nkhani yokambirana. Kambirananinso, mwachidule nkhani yomwe ili patsamba 2 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akulandira munthu yemwe wabwera ku Chikumbutso.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero