Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira February 24, 2014.
Kodi Satana anachititsa Hava kuti aziganizira kwambiri za chiyani ndipo pamene Hava anadya chipatso choletsedwacho anasonyeza chiyani? (Gen. 3:6) [Jan. 6, w11 5/15 tsa. 17 ndime 5]
N’chiyani chinathandiza Abele kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo zotsatira zake zinali zotani? (Gen. 4:4, 5; Aheb. 11:4) [Jan. 6, w13 1/1 tsa. 12 ndime 3; tsa. 14 ndime 4-5]
Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti asamasirire “ziphona” ndi “amuna otchuka” m’dzikoli? (Gen. 6:4) [Jan. 13, w13 4/1 tsa. 13 ndime 2]
Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Loti ndi mkazi wake yomwe ikupezeka pa Genesis 19:14-17, 26? [Jan. 27, w03 1/1 tsa. 16-17 ndime 20]
Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira zoti akufa adzauka komanso zoti mbewu yolonjezedwa idzachokera mwa Isaki? (Gen. 22:1-18) [Feb. 3, w09 2/1 tsa. 18 ndime 4]
Kodi tikuphunzira chiyani pa ulosi wa pa Genesis 25:23, umene umati “wamkulu adzatumikira wamng’ono”? [Feb. 10, w03 10/15 tsa. 29 ndime 2]
Kodi loto la Yakobo lokhudza “makwerero” limatanthauza chiyani? (Gen. 28:12, 13) [Feb. 10, w04 1/15 tsa. 28 ndime 5]
N’chifukwa chiyani Labani ankafunitsitsa kupeza aterafi amene anabedwa? (Gen. 31:30-35) [Feb. 17, w04 6/1 tsa. 29 ndime 2]
Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene mngelo anayankha Yakobo pa Genesis 32:29? [Feb. 24, w13 8/1 tsa. 10]
Kodi ndi njira imodzi iti imene tingapewere mavuto ngati amene Dina anakumana nawo? (Gen. 34:1, 2) [Feb. 24, w01 8/1 tsa. 20-21]