Nyengo ya Chikumbutso Imatipatsa Mwayi Wowonjezera Utumiki
1. Kodi tili ndi zifukwa zotani zowonjezera utumiki wathu m’miyezi ya March, April ndi May?
1 Kodi mungawonjezere utumiki wanu m’nyengo ya Chikumbutso ikubwerayi? Madera ambiri, nyengo idzakhala ili bwino komanso maola amasana adzakhala otalikirapo kuposa usiku. Ofalitsa ena amene amapita kusukulu komanso kuntchito adzakhala ali patchuti ndipo angadzagwiritse ntchito nthawi imeneyi kulowa mu utumiki. Kuyambira pa April 2 tidzasangalala ndi ntchito yapadera yoitanira anthu kumwambo wa Chikumbutso womwe udzachitike pa April 17. Ndipo pambuyo pake tidzayesetse kukulitsa chidwi cha anthu amene adzabwere ku mwambowu powaitanira ku nkhani yapadera yomwe idzakambidwe mlungu woyambira April 25. Ndithudi, tili ndi zifukwa zambiri zowonjezera utumiki m’miyezi ya March, April, ndi May.
2. Kodi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zowonjezerera utumiki wathu ndi iti?
2 Upainiya Wothandiza: Kuchita upainiya wothandiza ndi njira yabwino kwambiri yowonjezera utumiki wathu. Popeza tonse timakhala otanganidwa, kuti tikwanitse kuchita zimenezi tifunika kukonzekereratu nthawi idakalipo komanso kusintha zochita zina ndi zina. (Miy. 21:5) Mukhoza kusunthira kutsogolo zochita zina ndi zina zosafunika kwambiri zimene mumachita nthawi zonse. (Afil. 1:9-11) Mungachite bwino kuuzako ena mumpingo kuti mukufuna kuchita upainiya, mwina nawonso angachite nawo upainiya wothandiza.
3. Kodi mabanja angakonze zotani kuti awonjezere utumiki wawo?
3 Mukamadzachita Kulambira kwa Pabanja mlungu wamawa, mudzakambirane zolinga zomwe muli nazo monga banja. (Miy. 15:22) Ngati mutagwirizana zikhoza kutheka kuti ena m’banjamo achite upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo. Bwanji ngati mukuona kuti zimenezi ndi zosatheka? Mungakonzebe zowonjezera utumiki wanu mwa kulowa mu utumiki masiku ena madzulo kapena kulalikira nthawi yochulukirapo kumapeto a mlungu.
4. Kodi tingapeze madalitso otani ngati titawonjezera utumiki wathu m’nyengo ino ya Chikumbutso?
4 Yehova amaona zonse zimene tikuchita kuti timutumikire ndipo amayamikira kudzimana kwathu. (Aheb. 6:10) Timasangalala tikakhala opatsa kwa Yehova komanso kwa anthu. (1 Mbiri 29:9; Mac. 20:35) Yesetsani kuwonjezera zimene mumachita mu utumiki m’nyengo ya Chikumbutso kuti mupeze chimwemwe chochuluka komanso madalitso amene amakhalapo.