Ndandanda ya Mlungu wa February 14
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 14
Nyimbo Na. 3 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 2 ndime 15-20, ndi bokosi patsamba 23 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 9–11 (Mph. 10)
Na. 1: Nehemiya 11:1-14 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mateyu 1:23 Amasonyeza Kuti Pamene Yesu Anali Padziko Lapansi Anali Mulungu?—rs tsa. 428 ndime 1 mpaka 3 (Mph. 5)
Na. 3: Njira Zimene Mulungu Amaonetsera Kukoma Mtima Kwake Kwakukulu—1 Pet. 4:10 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 12: Mmene Mungachezere Ndi Munthu Wosam’dziwa. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 62 mpaka 64. Funsani mwachidule wofalitsa amene amadziwika kuti ali ndi luso lotha kuyamba kukambirana ndi anthu akamalalikira mwamwayi kapena nyumba ndi nyumba.
Mph. 18: “Nyengo ya Chikumbutso Imatipatsa Mwayi Wowonjezera Utumiki.” Mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pambuyo pokambirana nkhaniyi, fotokozani dongosolo limene mwakonza lolowera mu utumiki wakumunda m’miyezi ya March, April, ndi May. Fotokozani ndandanda zimene anthu a m’mikhalidwe yosiyanasiyana angatsatire kuti azikwanitsa maola 50 pa mwezi. Funsani ofalitsa awiri kapena atatu amene anachita upainiya wothandiza chaka chatha m’nyengo ya Chikumbutso ngakhale kuti anali ndi zochita zambiri kapena anali ndi mavuto ena okhudza thanzi lawo.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero