Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda January 1
Werengani Genesis 2:16, 17. Kenako nenani kuti: “Anthu ena amanena kuti Mulungu ankadziwiratu zoti Adamu adzachimwa. Ena amaona kuti chenjezo la Mulungu likanakhala lachinyengo akanakhala kuti ankadziwiratu zoti adzachimwa. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani imene ikuyambira patsamba 13 ikufotokoza mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kudziwa zam’tsogolo.”
Galamukani! January
“Anthu ena amaona kuti anthu amakhala ndi chikhulupiriro pa nkhani za chipembedzo popanda zifukwa zomveka. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Malinga ndi zimene Baibulo limanena, munthu sayenera kukhulupirira zinthu popanda zifukwa zokwanira. [Werengani 1 Yohane 4:1.] Nkhani imene ikuyambira patsamba 28 ikufotokoza zimene tingachite kuti zimene timakhulupirira zizikhala ndi zifukwa zomveka.”
Nsanja ya Olonda February 1
“Masiku ano mabanja ambiri amasudzulana. Kodi mukuganiza kuti kwenikweni zimenezi zikuchitika chifukwa chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Palemba ili pali uphungu umene wathandiza mabanja ambiri. [Werengani 1 Akorinto 10:24.] Magazini iyi ili ndi malangizo 6 othandiza pa zimene amuna kapena akazi ambiri amadandaula komanso ikusonyeza mmene kutsatira mfundo za m’Baibulo kungatithandizire.”
Galamukani! February
“Zikuoneka kuti anthu ambiri ayamba kuchita chidwi ndi nkhani za mizukwa, afiti komanso matsenga. Kodi mukuganiza kuti kuchita nawo zamizimu kulibe vuto lililonse? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chenjezo ili limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. [Werengani Deuteronomo 18:10-12.] Magazini iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mizimu.”