Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’chaka cha 2010, m’Malawi muno munachitika Misonkhano Yachigawo yokwana 63. Misonkhanoyi inachitika mu Chichewa, Chitumbuka, Chiyao, Chitonga, Chingelezi ndi Chinenero Chamanja cha ku America. Chiwerengero cha anthu amene anapezeka pa misonkhano yonseyi ndi 225,855 ndipo anthu okwana 2,434 anabatizidwa m’madzi posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova. Zoonadi, galeta lakumwamba la Yehova likuyenda mwamphamvu pokwanitsa cholinga chake.