Zilengezo
Mabuku ogawira mwezi wa January: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati mwininyumba ali nalo kale, mungagawire buku lililonse la masamba 192 limene linatuluka chaka cha 1995 chisanafike. February: Gawirani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? April: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza, kuphatikizapo kwa anthu amene anabwera pa Chikumbutso kapena pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
◼ Kuyambira mwezi wa February, oyang’anira madera ayamba kukamba nkhani ya onse ya mutu wakuti “Kodi Choonadi Chimakhudza Bwanji Moyo Wanu?”