Ndandanda ya Mlungu wa February 21
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 21
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 3 ndime 1-9 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 12–13 (Mph. 10)
Na. 1: Nehemiya 13:15-22 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kukhala Wodzipereka Kwa Mulungu Yekha Kumatanthauza Chiyani?—Eks. 20:5 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Lemba la Yohane 5:18 Limatanthauza Chiyani?—rs tsa. 428 ndime 4 ndi 5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Yehova Sadzasiya Anthu Ake Okhulupirika. (Sal. 37:28) Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Yandikirani kwa Yehova, tsamba 285, ndime 14, mpaka tsamba 289, ndime 21. Pambuyo pokambirana zokumana nazo za abale zimene zili patsamba 287, pemphani omvera kufotokoza zimene aphunzirapo.
Mph. 10: Muzinena Mawu Omaliza Ogwira Mtima mu Utumiki Wakumunda. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 221, ndime 5, mpaka kumapeto kwa tsamba 222. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito imodzi kapena ziwiri zochokera m’bukuli.
Mph. 10: “Msonkhano Umene Umathandiza Atumiki Achikhristu.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani tsiku la msonkhano wanu wadera ngati mukulidziwa. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene msonkhano wadera waposachedwapa unawathandizira.
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero