Msonkhano Umene Umathandiza Atumiki Achikhristu
1. Kodi ndi dongosolo latsopano lotani limene linayamba mu chaka cha 1938, nanga cholinga chake chinali chotani?
1 Mu 1938, gulu la Yehova linakhazikitsa dongosolo latsopano. Mipingo yambiri inayamba kusonkhana pamodzi kuti izisangalala ndi misonkhano yadera. Kodi cholinga cha misonkhano imeneyi chinali chotani? Kalata Yathu ya Mwezi ndi Mwezi (yomwe tsopano timati Utumiki Wathu wa Ufumu) ya January 1939 inati: “Misonkhano imeneyi ndi mbali ya zimene Yehova akuchita potsogolera gulu lake lomwe likutumikira Ufumu wake. Malangizo amene amaperekedwa pa misonkhano imeneyi ndi ofunika kwambiri kwa munthu aliyense kuti athe kugwira bwino ntchito imene wapatsidwa.” Chiwerengero cha olengeza Ufumu m’chaka chimenechi cha 1938, chinali 58,000 yokha basi. Ndipo tikaona mmene chiwerengerochi chawonjezekera pofika lero, timakhulupirira kuti misonkhano yaderayi ikukwaniritsadi cholinga chake, chomwe ndi kuthandiza atumiki ‘kugwira bwino ntchito imene apatsidwa.’
2. Kodi pamsonkhano wathu wadera padzakambidwa nkhani zotani?
2 Mutu wa Chaka Chino: Tikuyembekezera mwachidwi kudzasangalala komanso kulimbikitsidwa ndi pulogalamu imene iyambe m’mwezi wa April. Mutu wa msonkhano wadera wa chaka chino ndi wakuti “Simuli Mbali ya Dzikoli” ndipo wachokera pa Yohane 15:19. Kodi ndi mitu iti ya nkhani imene ikuoneka kuti idzathandiza kwambiri atumiki achikhristu? Loweruka tidzamvetsera nkhani yakuti “Kodi Utumiki wa Nthawi Zonse Umatiteteza Motani?” Komanso tidzamvetsera nkhani yosiyirana yokhala ndi mbali zitatu ya mutu wakuti “Musaipitsidwe ndi . . . ” “Chilombo,” “Hule Lalikulu,” ndiponso “Amalonda Oyendayenda.” Lamlungu tidzakhala ndi nkhani ina yosiyirana ya mutu wakuti “Muzikonda Yehova, Osati Dziko.” Zina mwa nkhani zimene zidzakambidwe pamsonkhanowu ndi zakuti “Ufumu wa Khristu ‘Suli Mbali ya Dziko Lino,’” “Pitirizani Kukhala ‘Alendo Ndiponso Anthu Osakhalitsa M’dzikoli’” ndiponso yakuti “Limbani Mtima! Mungathe Kuligonjetsa Dziko.”
3. Kodi kupezeka pamsonkhano wadera kudzatithandiza motani?
3 Mlongo wina yemwe anali atachepetsa changu chake mu utumiki, analemba kalata yoyamikira pambuyo popezeka pamsonkhano wadera waposachedwapa. Iye ananena kuti msonkhanowu unamuthandiza kuonanso mmene zinthu zilili pa moyo wake ndiponso kutsimikiza mtima kuti “azilowa mu utumiki mokhazikika ndi kusiya kupereka zifukwa zodzikhululukira.” Sitikukayika kuti msonkhano wadera wa m’chaka chautumiki chatsopano chimenechi utithandiza tonse kukonda Yehova m’malo mokonda dziko. (1 Yoh. 2:15-17) Yesetsani kuti mudzapezeke pamsonkhanowu komanso kuti muzidzamvetsera mwatcheru n’cholinga choti mudzapindule mokwanira ndi mphatso yachikondi imeneyi yomwe ndi yothandiza kwa atumiki achikhristu.