Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
Mu “nthawi zowawitsa” zino tikufunikira nzeru za Mulungu kuti tikhale ovomerezeka kwa Yehova ndi kuti iye apitirize kutiyanja. (2 Tim. 3:1) Msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2005, udzatipatsa malangizo othandiza ndi kutilimbikitsa pamene udzafotokoza mutu wakuti “‘Nzeru Yochokera Kumwamba’ Izikutsogolerani.”—Yak. 3:17.
Nkhani yosiyirana yoyamba ya mutu wakuti “Kuonetsa ‘Nzeru Yochokera Kumwamba’ Pamoyo Wathu,” idzatithandiza kumvetsa kuti zimatanthauzanji kukhala woyera, wamtendere, wololera, komanso wokonzeka kumvera bwino. Kenako, woyang’anira dera adzafotokoza mbali zina zitatu za nzeru zochokera kumwamba. Patsiku loyambali, woyang’anira chigawo adzamaliza ndi nkhani yofotokoza mmene atumiki achikristu alili okonzekeretsedwa bwino kulankhula nzeru za Mulungu, ngakhale kuti ena amawaona kuti ndi “osaphunzira ndi opulukira.”—Mac. 4:13.
Tsiku lachiwiri, nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Chitani Zinthu Zomangirira” idzatithandiza kuzindikira zinthu zimene zingatifooketse mwauzimu ndiponso kuzipewa kwake. Idzatithandizanso kuona mmene tingalimbitsire chikhulupiriro cha ena pa misonkhano ya mpingo, mu utumiki wa kumunda, komanso m’banja. Nkhani ya onse yakuti, “Mmene Timapindulira ndi Nzeru za Mulungu,” idzatithandiza kuyamikira kwambiri phindu limene timapeza tikamagwiritsa ntchito mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino pa moyo wathu. Nkhani yomalizira yakuti “Kutsatira Nzeru za Mulungu Kumatiteteza,” idzalimbitsa chosankha chathu chopempha nzeru kwa Yehova m’masiku otsiriza ano.
Chochitika chosangalatsa pa msonkhano uliwonse ndi ubatizo wa ophunzira atsopano. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu umenewo zidzachitikanso ku msonkhanowo. Yehova amafunitsitsa kuti tonse tipindule ndi nzeru zimene amapereka. Malangizo pamodzi ndi chilimbikitso zimene zidzaperekedwa ku msonkhano wadera zidzatilemeretsa mwauzimu.—Miy. 3:13-18.