Kubwereza Zophunziridwa pa Msonkhano Wadera
Nkhani ino ndiyoti itithandize kuona zimene tikaphunzire ku msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2005 komanso tidzaigwiritsa ntchito pobwereza zimene tikaphunzirezo. Nkhani ya mutu wakuti “Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera” imene ili pa tsamba 4 la mphatika ino ikufotokoza mmene tizichitira kubwerezaku. Pobwerezapo, gawani bwino nthawi kuti mukambirane mafunso onse. Pobwerezapo tsindikani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimene tinaphunzira kumsonkhanoko.
CHIGAWO CHAM’MAWA TSIKU LOYAMBA
1. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupeza nzeru yochokera kumwamba?
2. Kodi ndi khama lotani limene abale m’derali achita kuti afikire anthu ochuluka ndi uthenga wabwino?
CHIGAWO CHAMASANA TSIKU LOYAMBA
3. N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kukhala osadetsedwa mu mtima? Kodi timafunika kuchitanji kuti tikwanitse zimenezi?
4. Kodi tingakhale bwanji pa mtendere ndi abale anthu?
5. Kodi kukhala ololera n’kutani, ndipo tingakusonyeze bwanji ndi mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu?
6. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zitsanzo za Sauli ndi Nowa? Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzeka ‘kumvera bwino’? (Yak. 3:17)
7. Akristu angapewe motani kukhala ndi moyo wa chiphamaso?
8. Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Paulo poyankhula nzeru za Mulungu?
CHIGAWO CHAM’MAWA TSIKU LACHIWIRI
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala posankha zinthu zimene timachita, ndipo n’chiyani chidzatithandiza kuchita zimenezo?
10. Kodi ndi khama lotani limene ofalitsa m’derali akuchita kuti azipezeka pamisonkhano mokhazikika, ndipo apindula motani chifukwa chochita zimenezi?
11. Kodi mitu ya mabanja ingamange bwanji mabanja awo?
12. Kodi anatchula kuti dera lathu lili ndi zosowa ziti?
CHIGAWO CHAMASANA TSIKU LACHIWIRI
13. Monga kunanenedwera m’nkhani ya anthu onse, kodi ndi ntchito zolungama ziti zimene nzeru yochokera kumwamba yachita?
14. N’chifukwa chiyani kuli kupusa kudzidalira kapena kudalira aja amene satsogozedwa ndi nzeru za Mulungu? Ndi mbali ziti zimene tiyenera kukhala tcheru?
15. Kodi nzeru za Mulungu zimatiteteza ku mbuna ziti?
16. N’chifukwa chiyani ifeyo tikufunika kugwiritsa ntchito malangizo amene tinalandira pa msonkhano wadera?