Kubwereza Zophunziridwa pa Tsiku la Msonkhano Wapadera
Nkhani ino ndiyoti itithandize kuona zimene tikaphunzire pa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2005 komanso pobwereza zimene tikaphunzirezo. Nkhani ya mutu wakuti “Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera” imene ili pa tsamba 4 la mphatika ino ikufotokoza mmene tizichitira kubwerezaku. Gaŵani bwino nthaŵi pobwerezapo kuti mukambirane mafunso onse. Pobwerezapo tsindikani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimene tinaphunzira kumsonkhanoko.
CHIGAWO CHAM’MAWA
1. N’chifukwa chiyani nthaŵi zonse pali kufunika komvera Yehova akamalankhula? Kodi kumvera kumatanthauza chiyani? (“Chifukwa Chake Tiyenera Kumvera Mawu a Yehova”)
2. Kodi mabanja angatani kuti akhalebe ndi pulogalamu yabwino yochita zinthu zauzimu? (“Mabanja Amene Amamvetsera Mawu a Mulungu Popanda Zododometsa”)
3. Kodi abale agwiritsa ntchito motani mipata yolalikira mwamwayi m’dera lathuli? (“Kuchita Zonse ku Ulemerero wa Mulungu”)
4. Kodi tikutengapo phunziro lanji pa chitsanzo chotichenjeza chimene chikupezeka m’machaputala 3 ndi 4 a buku la Ahebri? Nanga Yehova akulankhula nafe m’njira iti masiku ano? (“Kumvera Mulungu Akamalankhula Kumatiteteza”)
5. Munapindula motani ndi nkhani yaubatizo? (“Kudzipatulira ndi Ubatizo”)
CHIGAWO CHAMASANA
6. Kodi tingazindikirenji za Yesu pamene anali mnyamata, nanga achinyamata m’dera lino akumutsanzira motani? (“Mmene Kumvetsera Mwatcheru Kumalimbikitsira Achinyamata Athu”)
7. Ndi njira zina ziti zimene makolo angayambe kugwiritsa ntchito pophunzitsa makanda ndi ana ang’ono njira za Yehova? (“Ana Aang’ono Amene Amamvera Mulungu Ndiponso Amene Amaphunzira”)
8. Kodi ndi m’zinthu zina ziti zimene tiyenera kumvera Yehova, Mwana wake, ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Mat. 24:45) N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tichite zimenezi? (“Mverani Malangizo a Mulungu Nthaŵi Zonse”)