Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Ngati tiona kapena kumva chenjezo koma osafuna kuchitapo kanthu mogwirizana ndi chenjezolo, zotsatirapo zake zingakhale zangozi kwambiri. Ndipotu n’kofunikadi kwambiri kuti tizichitapo kanthu pa malangizo auzimu amene Yehova amatipatsa. Izi n’zimene zidzafotokonzedwa bwino pa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki chimene chikudzachi. Mutu wa msonkhanowu ndi wakuti “Yang’anirani Mamvedwe Anu.”—Luka 8:18.
M’nkhani yake yoyamba, mlendo adzafotokoza mmene malangizo amene Paulo anauziridwa kulemba m’machaputala oyambirira a kalata yopita kwa Ahebri amatikhudzira lerolino. Mu nkhani yomalizira ya mutu wakuti “Mverani Malangizo a Mulungu Nthaŵi Zonse,” mlendoyu adzathandiza aliyense kudziona ngati amamveradi Yehova, Mwana wake, ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mat. 24:45.
Nkhani zingapo zimene zidzakambidwe pa msonkhanowu zidzakhala zothandiza mwapadera kwa mabanja. “Mabanja Amene Amamvetsera Mawu a Mulungu Popanda Zododometsa,” ndi mutu wa nkhani imene idzatithandiza kupeŵa zinthu za m’dzikoli zimene zingatilepheretse kukula mwauzimu. Padzakhalanso kufunsa awo amene asintha zinthu pa moyo wawo kuti athe kuika zinthu zauzimu pa malo oyamba. Nkhani yakuti “Mmene Kumvetsera Mwatcheru Mawu a Mulungu Kumalimbitsira Achinyamata Athu,” idzaphatikizapo kufunsa achinyamata amene akhala okhulupirika pa choonadi kusukulu, pakati pa mabwenzi awo, kapena mu utumiki. “Ana Aang’ono Amene Amamvera Mulungu Ndiponso Amene Amaphunzira,” ndi nkhani imene idzatithandiza kuti tisamaderere luso la ana aang’ono lokhoza kuphunzira zinthu. Kufunsa ana aang’ono pamodzi ndi makolo awo kudzatithandiza kuona ubwino wophunzitsa ana njira za Yehova kuyambira pa ubwana wawo.
Pamene Satana ‘akunyenga dziko lonse,’ Yehova akuonetsa atumiki ake okhulupirika njira imene afunika kuyendamo. (Chiv. 12:9; Yes. 30:21) Kumvera malangizo ake mwatcheru ndi kuwagwiritsa ntchito mokhulupirika pa moyo wathu kudzatichititsa kukhala anzeru, achimwemwe komanso kudzatitsogolera kumoyo wosatha.—Miy. 8:32-35.