Phunziro 5
Khalani Mmvetseri Wabwino
1-5. Kodi kumvetsera kumatanthauzanji, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika, makamaka pamisonkhano yampingo?
1 Kupita kwanu patsogolo monga mtumiki wa Yehova kumadalira kwambiri kumvetsera kwanu. Pamoyo wanu wonse kumvetsera kumathandiza kwambiri pophunzira zinthu. Mumamvetsera pamene mumva ndi maganizo osamalitsa, koma ngati maganizo anu sanasumikidwe pa zimene zikunenedwa, mawu amene akulankhulidwa amagwera pamakutu ogontha. Mosakayikira inu mwalankhulapo ndi anthu amene sanatchere khutu kwenikweni. Ngakhale kuti iwo kaŵirikaŵiri anali kuvomereza ndi mawu, inu munadziŵa kuti iwo sanali kumvetsa kwenikweni, motero sanapezepo phindu lenileni pazimene mumanena. Motero, tiyenera kukhala osamala chotani nanga kuti tikhale amvetseri abwino nthaŵi zonse, makamaka pamene tili pamaphunziro aumulungu! Monga momwe Miyambo 1:5 imanenera: “Wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira.”
2 Misonkhano ya mpingo ili gawo lina la pologalamu ya kuphunzitsa imene Yehova watipatsa kudzera mwa gulu lake. Mwa kumvetsera mosamalitsa timasonyeza ulemu kwa Yehova ndi makonzedwe ake a kutiphunzitsa. Koma Mulungu amadziŵa chipangidwe chathu ndi kuti nthaŵi zina tingalore maganizo athu kuyendayenda, choncho m’chiitano chake cha kudzadya chakudya chauzimu chochuluka chimene iye akuchipereka akutilangiza mogogomeza kuti: ‘Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, . . . Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, . . . mudzakhala ndi moyo.’ (Yes. 55:2, 3) Ngati tifuna moyo wamuyaya ndi kuthandiza enanso kupeza mfupo imeneyo, tifunikira kumvetsera mosamalitsa ndi kumvetsetsa malingaliro a Mulungu.—Aheb. 1:1, 2; 2:1.
3 Kumvetsera mosamalitsa kumasonyezanso kudzichepetsa koyenera, ndipo n’kofunika kuti tonsefe tikhale odzichepetsa. Tonsefe tingaphunzire kwa munthu wina; palibe amene adziŵa zonse. Ngakhale ngati wolankhulayo satha kulankhula mosadodoma kapena ngati akusoŵeka luso linalake la kulankhula, kudzichepetsa kuyenera kutisonkhezera kupereka chithandizo ndi chilimbikitso mwa kukhala kwathu otchera khutu ndi olabadira zimene akunena. Ndi iko komwe, tidziŵa bwanji mwina angatchule lingaliro lina kapena tanthauzo limene silinafikepo m’maganizo mwathu! M’kamwa mwa ana, m’lingaliro lauzimu, Yehova angapereke kuunika.—Mat. 11:25.
4 Kumvetsera mosamala n’kofunika kwenikweni pamisonkhano ya mpingo chifukwa tifunikira kugwiritsa ntchito zimene timaphunzira. Umunthu watsopano tingauvale kokha mwa kupeza “chidziŵitso cholongosoka.” (Akol. 3:9, 10, NW) Koma ngati sitimvetsera mosamala, ngati tilephera kumvetsa mfundo zina, tingalephere kuzindikira bwino masinthidwe amene tifunikira kupanga pamoyo wathu, moti tingapinimbire mwauzimu. Ndiponso, n’kofunika kukhoza kupereka mayankho olondola pakubwereramo kwapakamwa kapena kolemba. Ngati zili choncho, n’koposa chotani nanga mu utumiki wakumunda, popatsa aliyense amene atifunsa chifukwa cha chiyembekezo chabwino kwambiri chimene tili nacho!
5 Pamene mukulitsa chizoloŵezi cha kumvetsera mosamala zimene zikulankhulidwa, mudzakulitsa luso lanu la kukumbukira zimene mumamva.
6-8. Kodi mungaletse bwanji maganizo anu kuyendayenda pamene nkhani ikukambidwa?
6 Kumvetsera kwabwino. N’kwapafupi kulola nkhani zina kuchotsa maganizo athu pamisonkhanopo. Tingayambe kuganizira zinthu zimene zachitika tsikulo kapena kuda nkhaŵa za chinthu china chimene tiyenera kuchita maŵa. Koma ngati wina sakumvetsera zimene zikunenedwa, nanga n’kwanji kukhalapo? Choncho, n’kofunika kuti aliyense wa ife akhale wodziletsa kuti maganizo akhale pamodzi. Aliyense ayenera kukhala ndi chidwi chopereka maganizo ake onse kunkhani imene ikukambidwayo, ndi kuletsa maganizo ake kuyendayenda. Ziyenera kukhala monga kuti munthuyo watseka makatani a maganizo kuti malingaliro ena osagwirizana ndi nkhani imene ikukambidwayo asaloŵemo. Kumeneko ndiko kusumika maganizo.
7 Njira yabwino yoletsera maganizo kuyendayenda kapena kulota uli maso ndiyo kulemba mfundo ndi malemba otchulidwa ndi mlankhuliyo. Lembani mfundo zachidule, chifukwa zochulukitsitsa zidzadodometsa maganizo anu, koma zoŵerengeka zidzakuthandizani kusumika maganizo. Mfundozo zingadzakhale zopindulitsa m’tsogolo. Koma, ngakhale ngati simudzazigwiritsanso ntchito, zimakuthandizani kusumika maganizo pazimene zikunenedwa. Mumakhala womwerekera m’nkhani yokambidwayo ndipo mungathe kutchula mfundo zazikulu za mlankhuliyo.
8 Pakukambirana kwa tsiku ndi tsiku mutha kudziŵa kuti winayo akumvetsera ngati afunsa mafunso anzeru pankhaniyo. Chomwechonso, pomvetsera nkhani yokonzekeredwa, umakhala umboni wakuti maganizo anu ali pankhaniyo ngati mukufunsa mafunso anzeru m’maganizo mwanu ndi kuona ngati mlankhuliyo adzawayankha. Mwa zinthu zina, dzifunseni nokha mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zoperekedwazo.
9. Kodi ndi motani mmene liŵiro lofulumira la kuganiza lingagwiritsidwire ntchito mopindulitsa pomvetsera nkhani?
9 Anthu ambiri amaganiza mofulumira koposa mmene mlankhuli wa nkhani angakambire, zimene zimapatsa mpata malingaliro ena kuloŵa m’maganizo. Kwapezeka kuti anthu ambiri amaganiza pafupifupi mawu 400 pa mphindi imodzi, koma amalankhula pafupifupi mawu 125 pa mphindi imodzi. Komabe, tingagwiritse ntchito liŵiro la kuganiza limeneli motipindulitsa ngati tisinkhasinkha nkhani yokambidwayo, kusankhamo mfundo zazikulu, kuzipendanso, ndi kuzikhomereza m’maganizo mwathu.
10, 11. Kodi kukhala ndi cholinga choyenera kungatithandize motani pa kumvetsera?
10 Njira ina yogwirira mfundo zofunika zimene mlankhuliyo akupereka ndiyo kumvetsera ndi cholinga chabwino. Tisamamvetsere ndi cholinga chotsutsa mfundo za mlankhuliyo ndi kakambidwe kake. M’sukulu yautumiki woyang’anira woikidwa ndiye ali ndi udindo wopereka uphungu. Choncho zimenezo zimapatsa enafe ufulu woti tisumike maganizo pa mfundo iliyonse yopindulitsa imene mlankhuli ali nayo.
11 Ndiponso, pamene woyang’anira sukulu apereka uphungu kwa ophunzira okamba nkhani, sikuli kopindulitsa kuti wophunzira wina n’kumaganiza zoti aone ngati akugwirizana ndi uphungu woperekedwawo kapena ayi. Koma kudzakhala kom’pindulitsa kudzifunsa ngati uphunguwo ungagwirenso ntchito kwa iye, ndi mmene angapindulire nawo. Choncho mwa kukhala mmvetseri wabwino, nkhani iliyonse yoperekedwa imam’thandiza kupita patsogolo m’malo moti angoyembekezera nkhani imene ati adzakambe.
12. Kodi ana angaphunzire motani kukhala amvetseri abwino?
12 Achinyamata ndi ana ang’ono ayeneranso kuphunzitsidwa kukhala omvetsera mosamala. Kumakhala kothandiza ngati iwo akhala limodzi ndi makolo awo kuti aziwayang’anira. Ngati akhoza kuŵerenga, zimawalimbikitsa ngati akhala ndi kope lawolawo la chofalitsa chophunziridwacho. Sibwino kuwalola kuŵerenga buku losagwirizana ndi pologalamuyo. Monga chowasonkhezera kumvetsera, auzeni kuti mukafika kunyumba mudzawafunsa zimene aphunzirapo. Ndipo ayamikireni mwachikondi ngati akumbukira kapena ngati alemba kanthu kena konenedwa kumsonkhanoko.—Deut. 31:12.
13, 14. Kodi kadyedwe kathu kangayambukire motani kumvetsera kwathu?
13 Kusumika maganizo kumakhala kosavuta ngati tipeŵa kudya kwambiri popita kumsonkhano, chifukwa kumapatsa tulo. Chifukwa chake n’chakuti nyonga yochuluka ya thupi imagwira ntchito yopukusa chakudyacho, ndipo yochepa yokha ndiyo imagwira ntchito yoganiza. Mphamvu ya maganizo itafooketsedwa choncho, munthu amangomvetsera mwaulesi zimene zikunenedwa, popanda kulabadira kapena kumvetsa kwenikweni, ndipo nthaŵi zina amaodzera ndi kugwa m’tulo.
14 Mwinamwake chofunika koposa ndicho kulinganiza zochita zanu kuti muzifika nthaŵi zonse kudzalandira malangizo operekedwa. Ophunzira pasukulu zambiri amaphonya makalasi ndi cholinga choti adzabwereremo m’nkhanizo paokha. Koma simungapindule ndi malangizo amene simunamve poperekedwa. Musalole achibale kapena anzanu kuti akuphonyetseni misonkhano. Fikamponi nthaŵi zonse kuti mudzamve choonadi chopatsa moyo chochokera m’Mawu a Mulungu.
15, 16. Fotokozani mmene tingayesere ndi kukulitsa luso lathu la kumvetsera pamisonkhano.
15 Kuyesa luso lanu la kumvetsera. Timawonongera maola asanu mlungu uliwonse pamisonkhano yampingo, ndipo m’nthaŵi imeneyo timakhala ndi mwayi waukulu wa kuphunzira mwa kumvetsera. Kodi inuyo nthaŵiyo mumaigwiritsa ntchito bwino kwambiri? Kodi ndi mfundo zabwino zingati zimene mumakumbukira mlungu uliwonse m’nkhani zokambidwa? Itatha Sukulu Yateokalase ndi Msonkhano wa Utumiki, kodi mutha kufotokoza mfundo yaikulu ya nkhani iliyonse m’mawu anu, kapena kodi mumaona kuti nthaŵi zina simutha kukumbukira ngakhale amene anali papologalamu? Kodi mungapindule kwambiri mwa kuyesayesa mokulirapo kumvetsera, mwina ngakhale kulemba notsi? Yesani Zimenezo. Ndiyeno kambiranani ndi ena mfundo zazikulu pambuyo pamisonkhano.
16 Pamisonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu, kaŵirikaŵiri mafunso amafunsidwa ndipo omvetsera amapemphedwa kuyankha. Mayankho amenewo kaŵirikaŵiri amasonyeza kuti iwo anatayirapo maola ambiri paphunziro laumwini ndi kuti ali ndi zaka zambiri za chidziŵitso. Pamene ena apereka mayankho, kodi mumamvetseradi zimene iwo alikunena? Kodi mumamvetsera mosamalitsa kwambiri kotero kuti, pamene iwo amaliza, mukhoza kubwereza m’mawu anu mfundo yaikulu ya zimene iwo anena? Yesani kuchita zimenezo, ndipo mudzakondwera kuona kuti mumamva zambiri.
17. Kodi n’chiyani chingatithandize kusunga maganizo athu pamodzi pamene ndime zikuŵerengedwa?
17 Pamisonkhano imeneyi, kaŵirikaŵiri pamakhalanso kuŵerenga. Ndime za nkhani yophunzira zimaŵerengedwa pa phunziro la Nsanja ya Olonda ndi paphunziro la buku la mpingo. Kodi mumamvetseradi zimene zikuŵerengedwa, kapena mumalola maganizo anu kuyendayenda m’kati mwa kuŵerengako? Muli mfundo zochuluka m’ndime kwakuti nthaŵi silola kuti zonse zitulutsidwe ndi mayankho apakamwa. Ndipo kubwerezedwa kwa mfundo zazikulu kumathandiza kuzikhomereza m’maganizo. Inde, titha kuphunzira zochuluka ngati timvetseradi chilichonse chimene chikuŵerengedwa pamisonkhanoyo! Kudzakuthandizani kuchita zimenezo ngati musumika maso anu pazolembedwa m’buku ndi kumvetsera.
18-20. Kodi amvetseri achidwi amafupidwa motani?
18 Amvetseri achidwi amafupidwa. Amvetseri achidwi amazindikira kuti pali zophunzira zambiri ndipo amakhala ofunitsitsa kuphunzira zochuluka. Iwo amalabadira chilangizo cha pa Miyambo 2:3, 4, chakuti: ‘Itanitsa luntha, . . . fuulira kuti ukazindikire; . . . ifunefune ngati siliva.’ Ndipo pamene afunafuna, Yehova amawadalitsa, chifukwa iye walonjeza kuti: “Pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu. . . . Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.”—Miy. 2:5, 9.
19 N’zoona kuti kuti tikhale amvetseri abwino tiyenera kudziphunzitsa. Ndipo kumakhala kopindulitsa chotani nanga! Kukula kwathu kwauzimu kumakhala koonekera poyera. Timapanga masinthidwe opindulitsa m’moyo wathu. Ndipo luso lathu la kulengeza uthenga wabwino pa pulatifomu ndi mu utumiki wakumunda limawongokera.
20 Ngakhale kuti nthaŵi yathu ya phunziro laumwini ingakhale yochepa, tonse timakhala ndi mwayi womvetsera pamisonkhano yampingo. N’kofunika chotani nanga kuti tikhale ndi luso la kumvetsera! Ndipo popeza zinthu zimene timazimva zimaphatikizapo utumiki wathu kwa Yehova ndi moyo wathu wamuyaya, uli woyenerera chotani nanga uphungu wa Yesu wakuti: “Yang’anirani mamvedwe anu”!—Luka 8:18.