Yang’anirani Mamvedwe Anu
Kumvetsera mosamalitsa n’kofunika pamene tili pamisonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo. (Luka 8:18) Kodi mungawongolere bwanji luso lanu la kumvetsera?
◼ Peŵani kudya chakudya chambiri nthaŵi ya misonkhano itatsala pang’ono.
◼ Musalole maganizo anu kupita kwina.
◼ Lembani mwachidule mfundo zazikulu.
◼ Ŵerengani malemba amene akuŵerengedwa.
◼ Yankhani ngati papezeka mpata.
◼ Lingalirani nkhani imene ikukambidwayo.
◼ Ganizirani mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukumva.
◼ Pambuyo pake, kambiranani zimene mwaphunzira.
Onani Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase, phunziro 5.