Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera
Pamene dziko la Satana likuipiraipirabe, Yehova amatipatsa nyonga “kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.” (Tito 2:12) Zina mwa zinthu zimene iye amatipatsa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi misonkhano yadera komanso misonkhano yapadera yomwe imachitika chaka ndi chaka. (Mat. 24:45) Misonkhano yauzimu imeneyi imatilimbikitsadi kwambiri!
Potithandiza kuti tizikumbukira ndiponso kuti tizigwiritsa ntchito malangizo amene timalandira, m’chaka chautumiki cha 2005 tidzagwiritsa ntchito njira yatsopano pobwereza zophunziridwa pa misonkhanoyi. Pa tsamba 6 la mphatika ino pali nkhani yotionetsa zimene zidzakambidwa komanso mafunso amene tidzagwiritsa ntchito pobwereza za m’pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera. Mipingo idzakambirana mfundo zimenezi pa Msonkhano wa Utumiki kutatsala nthaŵi pang’ono kuti misonkhanoyi ichitike komanso itangochitika kumene. Kodi zimenezi zidzachitika motani?
Kutatsala mlungu umodzi kapena iŵiri kuti mpingo ukapezeke pa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera, nkhani ya mphindi 10 ya mutu wakuti “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera” idzakambidwa pa Msonkhano wa Utumiki pofuna kuti tiyembekezere msonkhanowo mwachidwi. Wokamba nkhaniyo adzafotokozanso za mafunso amene tidzagwiritsa ntchito pobwereza ndi kulimbikitsa omvetsera kukalemba notsi ku msonkhano pokonzekera kubwereza kumene kudzachitika milungu ingapo pambuyo pa msonkhanowo.
Pasanathe milungu ingapo mutachoka ku msonkhano, kwa mphindi 15 tidzabwereza mu Msonkhano wa Utumiki zimene tidzaphunzire pa tsiku lonselo la msonkhano. Mafunso amene tidzagwiritsa ntchito pobwereza omwe ali m’mphatika ino ndiwo adzakhala maziko a kukambiranako. Chinthu chachikulu pa kubwerezaku chiyenera kukhala kuona mmene mfundozo tingazigwiritsire ntchito. Akulu angakonze zoti nkhani zina za mu Msonkhano wa Utumiki zikambidwe mwachidule, azichotsepo, kapena adzazikambe m’tsogolo kuti pakhale nthaŵi yokwanira yochitira kubwerezaku.
Tizigwiritsa ntchito njira yofananayi pobwereza za msonkhano wadera kungopatulapo kuti patatha milungu yochepa kuchokera tsiku la msonkhanowo, pazikhala mphindi 15 zobwereza pulogalamu ya tsiku loyamba la msonkhano wadera pa Msonkhano wa Utumiki. Ndiyeno kwa mphindi 15 mlungu wotsatira, tizibwereza pulogalamu ya tsiku lachiŵiri la msonkhanowo. Tonsefe tiyenera kusamala mphatikayi ndi kuigwiritsa ntchito bwino kuti tipindule mokwanira ndi malangizo amene Yehova akupereka.—Yes. 48:17, 18.