Nyimbo 31
Ndife Mboni za Yehova!
1. Asema timilungu,
M’lungu wo’na sam’dziwa.
Ndiwamphamvuyonse
Monga tiona.
Milunguyo sidziwa
Zinthu zili m’tsogolo.
Milunguyinso si yoona
Ndipo ilibenso mboni.
(KOLASI)
Mboni za Yehovafe
Tinena mosaopa.
M’lungu wathu akalosera
Zinthu zimachitika.
2. Tilalikire dzina
La Yehova Mulungu.
Ndi Ufumu wake
Molimba mtima.
Ena amve cho’nadi
Kuti chiwamasule.
Akamalimba, adzaimba
Kutamanda nafe M’lungu.
(KOLASI)
Mboni za Yehovafe
Tinena mosaopa.
M’lungu wathu akalosera
Zinthu zimachitika.
3. Ntchito yolalikira
Za dzina la Yehova.
Imachenjezadi
Olidetsawo.
Imathandiza anthu
Kukhululukidwadi.
Imabweretsanso chimwemwe,
Ndiponso chiyembekezo.
(KOLASI)
Mboni za Yehovafe
Tinena mosaopa.
M’lungu wathu akalosera
Zinthu zimachitika.
(Onaninso Yes. 37:19; 55:11; Ezek. 3:19.)