Ndandanda ya Mlungu wa February 17
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 17
Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 7 ndime 14-20 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 29-31 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 29:21-35 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kuukitsidwa Kudzatanthauza Chiyani kwa Anthu Onse?—rs tsa. 110 ndime 1–tsa. 111 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Kalankhulidwe Ndiponso Khalidwe Lotani Limene Sililemekeza Ukwati?—lv tsa. 125-126 ndime 10-14 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Muzikhala Aubwenzi Mukamalalikira. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 118 ndime 1, mpaka 119 ndime 5.
Mph. 5: Kodi Mumagwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu ya jw.org/ny mu Utumiki? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene zinachitika pamene ankagwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org/ny mu utumiki. Limbikitsani omvera kuti aziuza anthu mu utumiki kuti azigwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org.
Mph. 15: “Zimene Mungachite Kuti Mudzasangalale M’nyengo ya Chikumbutso.” Mafunso ndi mayankho. Funsani amene akonza zoti adzachite upainiya wothandiza ngakhale kuti amadwaladwala kapena amapanikizika ndi ntchito. Apempheni kuti afotokoze zimene akonza n’cholinga choti adzakwanitse kuchita upainiya. Mukamakambirana ndime 3, funsani woyang’anira utumiki kuti afotokoze dongosolo limene mpingo wakonza lokhudza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda m’miyezi ya March, April ndi May.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero