Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Lembani Zokhudza Anthu Achidwi
“Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:16) Mawu a m’Baibulo amenewa, amene mtumwi Paulo analembera Timoteyo, akusonyeza kuti tiyenera kuyesetsa kuwonjezera luso lathu mu utumiki, kaya ndife atsopano kapena tinayamba kalekale choonadi. Pofuna kutithandiza kuchita zimenezi, mu Utumiki Wathu wa Ufumu muzikhala nkhani za mutu wakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki.” Nkhani iliyonse izitchula luso linalake limene tingawonjezere tikakhala mu utumiki ndipo izifotokoza mmene tingachitire zimenezi. Tonse tikulimbikitsidwa kuti mkati mwa mwezi umenewo, tiziyesetsa kuchita zimene nkhaniyo yanena. Kumapeto kwa mweziwo, mu Msonkhano wa Utumiki muzikhala nkhani imene izitipempha kufotokoza zimene takumana nazo komanso phindu limene tapeza potsatira malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki.” Mwezi uno tikulimbikitsidwa kuti tizilemba zokhudza anthu achidwi.
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’Kofunika? Kuti tikwaniritse ntchito imene tapatsidwa, tiyenera kuchita zambiri osati kulalikira kokha. Tiyenera kupitanso kwa anthu amene anasonyeza chidwi kuti tikawaphunzitse komanso kuti tikathirire mbewu za choonadi zimene tinabzala m’mitima yawo. (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 3:6-9) Kuti zimenezi zitheke, tifunika kukumananso ndi munthu amene tinacheza naye kale, kukambirana naye zimene zimamudetsa nkhawa komanso kupitiriza kucheza naye kuchokera pamene tinasiyira. Choncho tikapeza munthu wachidwi, ndi bwino kulemba zokhudza munthuyo.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukamalemba zokhudza munthu wachidwi, uzani amene mwayenda naye zimene mukulemba zokhudza munthuyo.