Bwererani kwa Onse Amene Asonyeza Chidwi Ngakhale Chochepa
1 Ambiri a ife tili m’choonadi lero chifukwa choti munthu wina anaona kuti tili ndi chidwi ndi uthenga wa Ufumu ndipo moleza mtima anabwereranso kwa ife, mwina kambirimbiri, kuti adzakulitse chidwicho. Nafenso tiyenera kubwereranso mokhulupirika kwa onse amene asonyeza chidwi, ngakhale chochepa. Ndipotu, kuchita maulendo obwereza ndi mbali imodzi ya ntchito yathu yoti ‘tikapange ophunzira.’—Mat. 28:19, 20.
2 Zindikirani Chidwi cha Munthu: Ngakhale ngati munthu sanalandire buku kapena magazini, nkhope yake, mawu ake, ndi zonena zake zingasonyeze kuti ali ndi chidwi ndithu ndi uthenga wa Ufumu. Pa chifukwa chimenecho, tingapange ulendo wobwereza. M’bale wina anapita kwa munthu winawake milungu isanu yotsatizana munthuyo osalandira buku lililonse. Pa ulendo wachisanu n’chimodzi, munthuyo analandira buku, ndipo kenaka phunziro la Baibulo linayambika.
3 Mukaona kuti munthu ali ndi chidwi, muzibwererako mwamsanga, mwina patatha masiku ochepa. Musapatse “woipayo” mpata woti achotse zimene mwafesa mumtima mwa munthuyo. (Mat. 13:19) Yesetsani kusunga lonjezo lanu ngati munalonjeza kuti mudzabwererako panthawi inayake.—Mat. 5:37.
4 Mu Ulaliki wa Mumsewu: Kodi mumayesetsa kusamalira chidwi chimene mumapeza pochita ulaliki wa mumsewu kapena polalikira mwamwayi? Pamapeto pa kukambirana kwanu, munganene kuti: “Ndasangalala kucheza nanu. Kodi ndingakupezeni kuti n’cholinga choti tidzachezenso?” Ngati zili zoyenerera, ofalitsa ena amapatsa munthu wachidwiyo nambala yawo ya foni kapena amamupempha kuti apatsane manambala a foni. Ngati anthu amakuonani mukulalikira pamsewu pamalo omweomwewo nthawi ndi nthawi, mwina sangakayike kukupatsani nambala yawo ya foni kapena kukuuzani kumene amakhala. Ngakhale atakana kukuuzani mmene mungawapezere, mukhozabe kuyesetsa kukulitsa chidwi chawo nthawi yotsatira yomwe mwakumana nawo pamsewu.
5 Tikaona maluwa amene tathirira ndi kutengulira akukula bwino, timasangalala. Mofanana ndi zimenezi, tikhoza kusangalala kwambiri mwa kupanga maulendo obwereza ndi kuthandiza anthu kupita patsogolo mwauzimu. (1 Akor. 3:6) Choncho khalani ndi cholinga chobwereranso kwa onse amene asonyeza chidwi, ngakhale chochepa.